Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 2/1 tsamba 3
  • Kodi Ndani Amakhulupirira Mizimu Yoipa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Amakhulupirira Mizimu Yoipa?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Zochita za Angelo Komanso Ziwanda Zimakhudzira Moyo Wathu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Lolani Kuti Yehova Akuthandizeni Polimbana ndi Mizimu Yoipa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Kodi Ziwanda N’zotani?
    Galamukani!—2010
  • Mizimu Yoipa Njamphamvu
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 2/1 tsamba 3

Kodi Ndani Amakhulupirira Mizimu Yoipa?

KODI mumakhulupirira kuti mizimu yosaoneka ingasonkhezere moyo wanu? Ambiri angayankhe mwamphamvu kuti ayi. Pamene kuli kwakuti amavomereza kukhalapo kwa Mulungu, iwo amatsutsa lingaliro la ochita zoipa okhala ndi mphamvu zoposa zaumunthu.

Kufalikira kwa kusakhulupirira mizimu m’maiko a Kumadzulo kumachititsidwa pang’ono ndi chiyambukiro cha Dziko Lachikristu, limene kwa zaka mazana ambiri linaphunzitsa kuti dziko lapansi linali phata la chilengedwe chonse, lokhala pakati pa thambo ndi helo wapansi pa nthaka. Malinga ndi kunena kwa chiphunzitso chimenechi, angelo anali ndi chimwemwe cha kukhala kumwamba pamene kuli kwakuti ziŵanda zinayendetsa zochitika za ku helo.

Pamene zotumbidwa za sayansi zinachititsa anthu kukana malingaliro olakwa onena za mpangidwe wa chilengedwe chonse, kukhulupirira zolengedwa zauzimu kunakhala kwachikale. The New Encyclopædia Britannica imanena kuti: “M’zochitika za pambuyo pa kusintha kwa Copernicus kwa m’zaka za zana la 16 (kozikidwa pa nthanthi za Copernicus, wopenda zakuthambo wa ku Poland), mmene . . . Dziko Lapansi silinaonedwenso monga phata la chilengedwe koma, mmalomwake, monga planeti wamba lokhala m’dongosolo la maplaneti ozungulira dzuŵa limene lili mbali yaing’ono kwambiri ya mlalang’amba m’chilengedwe chimene mwachiwonekere chili chopanda polekezera​—malingaliro a angelo ndi ziŵanda sanaonedwenso kukhala oyenerera.”

Pamene kuli kwakuti ambiri samakhulupirira mizimu yoipa, pali mamiliyoni ambiri amene amatero. Angelo ochimwa amachita mbali yaikulu m’zipembedzo zambiri, ponse paŵiri zakale ndi zamakono. Kuwonjezera pa thayo lawo la kuwononga mkhalidwe wauzimu, angelo oipa ameneŵa amaonedwa monga nthumwi za masoka, onga ngati nkhondo, njala, ndi zivomezi, ndiponso monga ochirikiza matenda, misala, ndi imfa.

Satana Mdyerekezi, mzimu woipa waukulu m’Chikristu ndi Chiyuda, amatchedwa Iblis ndi Asilamu. M’chipembedzo chakale cha ku Perisiya cha Zoroaster, amaonedwa monga Angra Mainyu. M’chipembedzo cha Gnostic, chimene chinafalikira m’zaka za zana lachiŵiri ndi lachitatu C.E., analingaliridwa kukhala Demiurge, dzina limene linaperekedwa kwa mulungu wansanje ndi wamng’ono amene unyinji wa mtundu wa anthu unamulambira mosadziŵa.

Mizimu yoipa yaing’ono imachita mbali yaikulu m’zipembedzo za Kummaŵa. Ahindu amakhulupirira kuti asuras (ziŵanda) amatsutsa devas (milungu). Amene amaopedwa kwambiri pakati pa asuras ndiwo a rakshasas, anthu owopsa amene amakhala kumanda.

Abuddha amalingalira ziŵanda kukhala mphamvu zokhala ndi maumunthu zimene zimaletsa munthu kufika ku Nirvana, kutha kwa chikhumbo. Wopereka chiyeso wamkulu pakati pawo ndiye Mara, ndi ana ake aakazi atatu otchedwa Rati (Chikhumbo), Raga (Chisangalalo), ndi Tanha (Kusakhazikika).

Olambira a ku China amagwiritsira ntchito moto woyatsidwa pabwalo, miyuni, ndi makombola kudzichinjiriza kwa kuei, kapena ziŵanda za chilengedwe. Zipembedzo za ku Japan nazonso zimakhulupirira kuti pali ziŵanda zambiri, kuphatikizapo a tengu owopsawo, mizimu imene imaloŵa mwa anthu kufikira itatulutsidwa ndi wansembe.

Pakati pa zipembedzo zopanda zolembedwa za ku Asia, Afrika, Oceania, ndi ku Americas, zolengedwa zauzimu zimakhulupiriridwa kukhala zothandiza kapena zovulaza malinga ndi mikhalidwe ndi maganizo awo panthaŵiyo. Anthu amalambira mizimu imeneyi kuti apitikitse tsoka ndi kulandira chiyanjo.

Wonjezerani ku zonsezi kufalikira kwa kukondwerera matsenga ndi kulambira mizimu, ndipo kuli kwachionekere kuti kukhulupirira mizimu yoipa kuli ndi mbiri yaitali ndi yoipa. Koma kodi nkwanzeru kukhulupirira kuti zolengedwa zoterozo ziliko? Baibulo limati ziliko. Komabe, ngati zilikodi, kodi nchifukwa ninji Mulungu amazilola kusonkhezera munthu kuti adzivulaze?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena