Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 4/1 tsamba 32
  • Kufalitsidwa Pamodzi kwa Zaka Khumi!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufalitsidwa Pamodzi kwa Zaka Khumi!
  • Nsanja ya Olonda—1994
Nsanja ya Olonda—1994
w94 4/1 tsamba 32

Kufalitsidwa Pamodzi kwa Zaka Khumi!

Pamene mlongo wokondedwa Wachisipanishi anafunsidwa mmene anamvera zaka khumi zapitazo pamene Nsanja ya Olonda Yachisipanishi inayamba kufalitsidwa pamodzi ndi Yachingelezi, anayankha kuti: ‘Timaona kuti ndidalitso chifukwa chakuti tsopano tili pa, mumati bwanji, sitepe limodzi ndi Chingelezi. Pamene ndikuti Chingelezi, nthaŵi zonse ndimaganiza za gulu [la Yehova]. Timatcha gululo monga “Amayi.” Timamva kukhala oyandikana nalo, kukhala nalo pafupi kwambiri. Nzabwino kwabasi. Nzokondweretsa zedi!’

Mlongo wokhulupirika ameneyu anasonyeza malingaliro a anthu ambiri osaŵerenga Chingelezi. M’zaka zakumbuyoku, nkhani zinaonekera mu Nsanja ya Olonda Yachisipanishi patapita miyezi pafupifupi isanu ndi umodzi zitafalitsidwa kale m’Chingelezi. Zinenero zinanso zinali ndi kuchedwa kofananako. Momvekera bwino, panali chikhumbo chachikulu cha kufalitsa nkhani zofanana, panthaŵi imodzimodzi, m’zinenero zambiri.

Chotero kuyamba ndi kope la April 1, 1984, magazini Yachisipanishi inali yoyamba kufalitsidwa pamodzi ndi Yachingelezi. Zinenero zina zinatsatira posapita nthaŵi. Poyamba chaka cha 1985, makope m’zinenero 23 anali kufalitsidwa pamodzi ndi Chingelezi. Pamene otembenuza anapezedwa ndi kuphunzitsidwa, makope m’zinenero zowonjezereka anagwirizana ndi Chingelezi.

Kope lino la Nsanja ya Olonda ndilo la chaka cha khumi cha kufalitsidwa pamodzi. Nsanja ya Olonda tsopano ikufalitsidwa m’zinenero 116, mwa zimene 85 zimafalitsidwa pamodzi ndi Chingelezi. Izi zikutanthauza kuti 99.3 peresenti ya avareji yonse yotulutsidwa ya makope 16,100,000 a Nsanja ya Olonda imatulutsidwa ndi chikuto chofanana ndiponso nkhani zake. Kwa awo amene amafika pa Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu ndi mlungu, oposa pa 95 peresenti amaphunzira nkhani imodzimodzi panthaŵi imodzi.

Galamukani!, magazini inzake ya Nsanja ya Olonda, imafalitsidwa pamodzi ndi Chingelezi m’zinenero 37 mwa zinenero zake 74. Yearbook of Jehovah’s Witnesses yapachaka imafalitsidwa m’zinenero 18. Kufalitsidwa pamodzi m’zinenero zosiyanasiyana koteroko kumagwirizanitsa anthu a Mulungu “m’maganizo amodzimodzi ndi njira ya kulingalira imodzimodzi.”​—1 Akorinto 1:10, NW.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena