Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 4/15 tsamba 32
  • A Mtengo Woposa wa Ngale

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • A Mtengo Woposa wa Ngale
  • Nsanja ya Olonda—1994
Nsanja ya Olonda—1994
w94 4/15 tsamba 32

A Mtengo Woposa wa Ngale

Ziŵerengero zowonjezereka za alendo amasangalala kuona zinthu zonga izi m’madzi a Nyanja Yofiira.

Nsomba zosaŵerengeka za mitundu ndi maonekedwe osiyanasiyana zimasangalatsa awo amene amasambira m’madzi oyera. Koma onani kuti m’mbali mwa nsomba zokongola zomwe zikuonekera pano, muli zinthu zina zokongola za m’madzi, kuphatikizapo ngale zokhala ndi maonekedwe oŵala.

Ngale zokongolazo zimapezeka m’mipangidwe ndi mitundu yambiri. Monga momwe mungayerekezere, ngakhale m’nthaŵi zamakedzana zidutswa zokongola za ngale zinali za mtengo wapatali. Akatswiri a ntchito yamanja anali kupanga zokometsera zokongola, ndipo olemba Baibulo anatchula ngale pamodzi ndi golidi, siliva, ndi rubi. (Miyambo 3:14, 15; Ezekieli 27:16, NW) Koma olembawo akutithandiza kuona zoposa kukongola ndi mtengo wa ngale zenizenizo.

Iwo amagogomezera kuti zinthu zina ndi zamtengo koposa ndipo tiyenera kuziona kukhala zamtengo kwambiri. Mkazi wabwino, waluntha ali mmodzi wa izo, popeza timaŵerenga kuti: “Mkazi wangwiro ndani angampeze? Pakuti mtengo wake uposa ngale.” (Miyambo 31:10) Kodi ndinu mwamuna wokwatira? Tayang’ananinso ngale zokongolazi, ndipo onani ngati mukupatsa mkazi wanu mtengo womwe amayenerera.

Kaya ndife amuna kapena akazi, okwatira kapena osakwatira, kaonekedwe ka ngale zokongola kayenera kutithandiza kuyamikira mokulira kwambiri mtengo wa nzeru yaumulungu, kuzindikira, ndi chidziŵitso. Mawu a Mulungu amati: “Wodala ndi wopeza nzeru, ndi wowona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golidi woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.”​—Miyambo 3:13-15; 8:11.

Chotero kaya tikuziona mwa kusambira kapena pachithunzithunzi, ngale za m’Nyanja Yofiira ziyenera kutidziŵitsa ponse paŵiri kukongola ndi zinthu zopindulitsa zoyenera kuzilingalira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena