‘Tsamba Limodzi Lingachotse Mdima Mofanana ndi Nyenyezi’
LEROLINO, matembenuzidwe a Malemba Opatulika amapezeka pafupifupi padziko lonse. Komabe, kaŵirikaŵiri nkhondo yolimbana ndi Baibulo inali ya moyo ndi imfa.
M’buku lakuti Fifteenth Century Bibles, Wendell Prime analemba kuti: “Zaka makumi atatu pambuyo pa kutumbidwa kwa kusindikiza, Bwalo Lopereka Chilango linali kugwira ntchito mwachipambano kwambiri mu Spain. Mwa anthu 342,000 amene linalanga m’dziko limenelo 32,000 anawotchedwa amoyo. Linali Baibulo limene linawachititsa kukhala owotchedwera chikhulupiriro. Chiwiya chokhaulitsira chimenechi chinalinso chowopsa kumpoto ndi kummwera komwe kwa Italy. Maakibishopu, mothandizidwa ndi Bwalo Lopereka Chilango, anali moto wonyeketsa Mabaibulo ndi owaŵerenga omwe. Nero anapanga Akristu ena kukhala miyuni m’dziko mwa kuwawotcha pamoto, atasokereredwa m’matumba, atapakidwa phula, kuwagwiritsira ntchito monga makandulo kuŵalitsira mapwando ake oipa. Koma makwalala a mizinda ya ku Ulaya anaŵala ndi moto wa Baibulo. Mabaibulo sanali ngati oŵerenga amene akanasautsidwa, kuvulidwa, kuzunzidwa, kuchekedwa nthulinthuli ndi kuonedwa monga osafunidwa. Ngakhale tsamba lopulumuka lingachotse kuda kwa mdima uwu monga nyenyezi.” (Kanyenye ngwathu.)
Zimene mlembi Prime akulongosola zinachitikadi m’nkhani ya tsamba la Baibulo lotulutsidwanso pano. Ndi tsamba la colophon, ndiko kuti, tsamba lomalizira la buku lokhala ndi malembo ozindikiritsa wotembenuza wake. Madanga aŵiri oima moyandikana pamwambapa ali mavesi omalizira a Apocalypse, kapena buku la Chivumbulutso.
Ponena za buku limeneli, The Cambridge History of the Bible limanena kuti: “Matembenuzidwe a Catalan ochitidwa ndi Bonifacio Ferrer a Baibulo anasindikizidwa mu Valencia, mu 1478; makope onse amene analipo anawonongedwa ndi Bwalo Lopereka Chilango isanafike 1500, koma tsamba limodzi lokha lidakalipo mu laibulale ya Hispanic Society of America.” (Kanyenye ngwathu.)
Wendell Prime ananenanso kuti: “Kwa atsogoleri achipembedzo ochita manthawo kunalibe Mabaibulo abwino koma Mabaibulo akupsa. Moto wopatulika umenewu ukanaunikira kwambiri koma kunalibe zokolezera. M’malo ambiri kunalibe moto wa Baibulo kokha chifukwa chakuti akuluakulu anali akhama kwambiri kwakuti kunalibe Mabaibulo oti awotchedwe.” Mosasamala kanthu za zoyesayesa zakhama zimenezi za kuchotseratu Mabaibulo omwe analinganizidwira anthu wamba, makope ambiri anapulumuka chiwonongekocho. Prime anawonjezera kuti: “Mabaibulo anasungidwa mwa kutengedwa ndi othaŵa, kapena mwakubisidwa ngati miyala ndi zitsulo zamtengo wake m’nthaŵi za mavuto ndi ngozi.”
Yesaya mneneri wa Mulungu analemba kuti: “Anthu onse ndi udzu . . . Udzu unyala, duwa lifota, koma mawu a Mulungu wathu adzakhala nthaŵi zachikhalire.” (Yesaya 40:6, 8) Mkati mwa zaka mazana ambiri, unyinji wa okonda Baibulo ndi otembenuza ambiri olimba mtima anadziika paupandu kwambiri ndipo anavutika kwambiri chifukwa cha Mawu a Mulungu. Komabe, zoyesayesa za anthu zokha sizikanakhoza kutsimikizira kusungidwa kwake. Timathokoza Mlembi wa Baibulo, Yehova, chifukwa cha kusungidwa kumeneku.
[Mawu a Chithunzi patsamba 7]
Courtesy of The Hispanic Society of America, New York