Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 6/15 tsamba 32
  • Abrahamu—Woikidwa Panopa, Komabe Wamoyo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Abrahamu—Woikidwa Panopa, Komabe Wamoyo?
  • Nsanja ya Olonda—1994
Nsanja ya Olonda—1994
w94 6/15 tsamba 32

Abrahamu​—Woikidwa Panopa, Komabe Wamoyo?

Kwa zaka mazana ambiri Ayuda, Asilamu, ndi Akristu ayenda ulendo kumka kumalo ameneŵa.

Mungapite kukawaona ku mzinda wakale wa Hebroni, kummwera kwa Yerusalemu. Chimango chimenechi chimatchedwa Haram el-Khalil ndiponso Manda a Makolo. Inde, pamenepa pamavomerezedwa ndi ambiri kukhala manda a makolowo Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, ndiponso akazi awo Sara, Rebeka, ndi Leya.

Kumbukirani m’Baibulo kuti pa imfa ya Sara, mkazi wake wokondedwayo, Abrahamu anagula manda a phanga ndi munda m’Makipela, pafupi ndi Hebroni. (Genesis 23:2-20) Pambuyo pake, Abrahamu nayenso anaikidwa panopo, monga momwe zinakhaliranso kwa ziŵalo zina za banja. Zaka mazana ambiri pambuyo pake, kuzungulira dera la manda a mwambolo, Herode Wamkulu anamanga nyumba yochititsa chidwi imene inasinthidwa m’kupita kwa nthaŵi ndi kukulitsidwa ndi ogonjetsa ena, akumasonyeza zikhulupiriro zawo zachipembedzo.

Mutaloŵa, mukhoza kuona zoumba zisanu ndi chimodzi (zikumbutso kapena manda opanda kanthu). Chithunzicho chikusonyeza chija cha Isake, mwana wa Abrahamu. Pafupi nacho pali ziboo zobooledwa pansipo, zimene zagwiritsidwa ntchito kuloŵera ku zinthu zimene zili pansipo. Ofufuza apeza zipinda zimene zingakhale zinali ndi mafupa ambirimbiri akale.

Bwanji za Abrahamu? Ngati anaikidwa m’phanga limene tsopano lili pansi pa malo ameneŵa, iye anafa kalekale, si choncho kodi? Alendo odzaona ambiri angavomereze. Komabe mneneri wina woposa Abrahamu ananena kuti m’lingaliro lina Abrahamu adakali moyo. Motani? Ndipo kodi ndi chiyambukiro chotani chimene zimenezi zingakhale nacho pa chikhulupiriro chanu?

Chonde ŵerengani nkhani yakuti “Akufa Anu Okondedwa​—Kodi Ali Kuti?” (Tsamba 3) Ikufotokoza zimene mneneri wamkuluyo ananena ponena za kukhalabe ndi moyo kwa Abrahamu, chidziŵitso chimene chingakhale chofunika kwambiri kwa inu ndi banja lanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena