Iwo Akugwirizana mu Umodzi Waubale
Panali pa August 7, 1993, pa Republican Stadium ku Kiev, Ukraine. Ofikapo oposa 64,000, anapenyerera ndi chiyembekezo pamene nthaŵiyo inafika. Ndiyeno, poyankha mafunso aŵiri ofunika, zikwi zinafuula kuti “Da!” (“Inde!”) Mwanjira imeneyi, iwo analengeza poyera chikhulupiriro chawo ndiyeno anapita kukasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova Mulungu mwa kubatizidwa m’limodzi la maiŵe asanu ndi limodzi m’sitediyamuyo.—Mateyu 28:19.
Motero, pa tsiku lachitatuli la Msonkhano wa Mboni za Yehova wa mitundu yonse wakuti “Chiphunzitso Chaumulungu,” omvetsera anaona chochitika chapadera: 7,402 anabatizidwa ndi kukhala mbali, osati ya tchalitchi chogawikana, koma ya mpingo Wachikristu wogwirizana wapadziko lonse.
Ngati mungakonde kuphunzira zowonjezereka ponena za umodzi weniweni Wachikristu, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera pandandanda ya patsamba 2.