Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 7/15 tsamba 25
  • Mapwando a Tsiku Lakubadwa Asiya Zotsatirapo za Imfa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mapwando a Tsiku Lakubadwa Asiya Zotsatirapo za Imfa
  • Nsanja ya Olonda—1994
Nsanja ya Olonda—1994
w94 7/15 tsamba 25

Mapwando a Tsiku Lakubadwa Asiya Zotsatirapo za Imfa

KUCHITA mapwando a tsiku lakubadwa kwaonedwa ndi anthu ochuluka lerolino kukhala mwambo wopanda choipa. Koma Baibulo silimapereka chithunzi chabwino cha mwambo umenewu. Choyamba, Malemba alibe umboni wakuti aliyense wa atumiki okhulupirika a Mulungu anachita mapwando a tsiku lakubadwa.

Masiku okha akubadwa amene Baibulo limatchula anali a olamulira amene anali adani a Mulungu. Phwando lililonse linaphatikizapo kupha, kotero kuti alendo akanakhoza kupenyerera imfa ya munthu amene anali atakwiyitsa mfumu. M’chochitika choyamba, Farao, mfumu ya Igupto, anapha wophika mkate wake wamkulu. (Genesis 40:2, 3, 20, 22) Wolamulira wa Iguptoyo anatero mkati mwa phwandolo chifukwa chakuti anali atakwiya ndi mtumiki wake. M’chochitika chachiŵiri, Herode, wolamulira wachisembwere wa Galileya, anadula mutu Yohane Mbatizi monga chosankha cha msungwana amene kuvina kwake paphwandopo kunamkondweretsa. Nzochitika zonyansa chotani nanga!​—Mateyu 14:6-11.

Komabe kodi sizangokhala kuti Baibulo langosankhapo masiku akubadwa aŵiri apadera kwambiri? Osati kwenikweni. Wolemba mbiri Wachiyuda wakale Josephus akuvumbula kuti zochitika zotero sizinali ziŵiri zokhazo. Amatchula zochitika zina za chizoloŵezi cha kupha pa masiku akubadwa kaamba ka kusanguluka.

Mwachitsanzo, zina zinachitika pambuyo pa kuwonongedwa kwa Yerusalemu mu 70 C.E., pamene Ayuda 1,000,000 anawonongeka ndipo 97,000 anapulumuka natengedwa undende. Ali paulendo wa ku Roma, kazembe wa Roma Titus anatengera akapolo ake Achiyuda kudoko lapafupi la Kaisareya.

Josephus akulemba kuti: “Pamene Titus anali ku Kaisareya, anachita phwando la tsiku lakubadwa la mbale wake Domitian ndi ulemerero waukulu, akumapha andende 2,500 m’maseŵera a zilombo ndi moto. Pambuyo pa zimenezi anapita ku Berytus [Beirut], gawo lolamulidwa ndi Roma ku Foinike, kumene anachitira phwando la tsiku lakubadwa la atate wake mwa kupha ogwidwa ukapolo owonjezereka pa zionetsero zazikulu.”​—The Jewish War, VII, 37, lotembenuzidwa ndi Paul L. Maier mu Josephus: The Essential Writings.

Nkosadabwitsa kuti The Imperial Bible-Dictionary imati: “Ahebri apambuyo pake anaona kuchita mapwando a tsiku lakubadwa monga mbali ya kulambira mafano, lingaliro limene lingatsimikiziridwe kwambiri ndi zimene anaona m’madzoma ofala ogwirizana ndi masiku ameneŵa.”

Akristu okhulupirika a m’zaka za zana loyamba sakanalingalira za kudziphatikiza m’mwambo wosonyezedwa moipa kwambiri m’Baibulo ndi wokondwereredwa monyansa ndi Aroma. Lerolino, Akristu oona mtima amazindikira kuti zolembedwa za Baibulo ponena za masiku akubadwa zinali pakati pa zinthu zolembedwera kuwalangiza. (Aroma 15:4) Amapeŵa kuchita mapwando a tsiku lakubadwa chifukwa chakuti madzoma otero amalemekeza munthu mosayenerera. Kwakukulukulu, atumiki a Yehova mwanzeru amalingalira za chithunzi choipa cha masiku akubadwa choperekedwa m’Baibulo.

[Chithunzi patsamba 25]

Bwalo la ku Kaisareya

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena