Kodi Ana Athu Ali ndi Mtsogolo Motani?
CHIWOPSEZO cha nyukliya—kaya kuchokera ku mabomba a zigaŵenga kapena ku ngozi zochitika pa magwero a mphamvu ya nyukliya—chili pa onse. Mungakhale mukudera nkhaŵa kwambiri kaamba ka ana, kuphatikizapo ana anuanu kapena adzukulu. Nzochititsa chisoni chotani nanga kuzindikira kuti chiwopsezo cha nyukliya chikuika paupandu thanzi ndi mtsogolo mwa mwana aliyense.
Koma musataye mtima. Pali chifukwa chakuti mukhale ndi lingaliro labwino la mtsogolo mwa ana. Maziko a chiyembekezo ali ozikidwa, osati pa zoyesayesa za munthu za kutetezera ana athu, koma pa mtsogolo mokhala m’manja mwa Mlengi wathu.
Pamene Mwana wa Mulungu, Yesu, anaphunzitsa ku Middle East, iye anasonyeza nkhaŵa kaamba ka ana. (Marko 9:36, 37, 42; 10:13-16) Baibulo limasonyeza kuti nkhaŵa yofananayo idzasonyezedwa pamene Mulungu pomalizira pake adzathetsa chiwopsezo cha nyukliya ndi kukhazikitsa paradaiso wa padziko lonse. Ana athu angasangalale ndi zimenezo, ndipo nanunso mungatero.
Ngati mungafune chidziŵitso chowonjezereka kapena kuti wina akufikireni kudzachititsa phunziro la Baibulo lapanyumba laulere kwa inu, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenerera yondandalikidwa patsamba 2.