Mawu Ozokota Okhala ndi Tanthauzo Lapadera
“IEHOVA SIT TIBI CUSTOS”
MAWU ameneŵa ozokotedwa pakhoma la kutsogolo la nyumba ya m’zaka za zana la 17 ku Celerina, kummaŵa kwa Switzerland, amatanthauza kuti “Yehova akhale mtetezi wanu.” M’dera la mapiri limeneli, sikwachilendo kupeza dzina la Mulungu lozokotedwa kapena kulembedwa pa nyumba, matchalitchi, ndi nyumba za ansembe za zaka mazana ambiri. Kodi ndimotani mmene dzina lakuti Yehova linakhalira lodziŵika kwambiri?
Rhaetia wakale (wophatikizapo mbali zimene tsopano zili kummwera koma chakummaŵa kwa Germany, Austria, ndi kummaŵa kwa Switzerland) anakhala chigawo cha Roma mu 15 B.C.E. Nzika zake zinayamba kulankhula Chiromanshi, chinenero chosanganikirana ndi Chilatini chimene chinakula kukhala zilankhulo zingapo zimene zikali kulankhulidwa m’zigwa zina za Alps za Switzerland ndi kumpoto kwa Italy.
M’kupita kwa nthaŵi, mbali za Baibulo zinatembenuzidwa m’Chiromanshi. Kope lina, Biblia Pitschna, linali ndi Masalmo ndi Malemba Achigiriki Achikristu. M’Baibulo limeneli, lofalitsidwa mu 1666, dzina lakuti Iehova linapezeka nthaŵi zambiri m’Masalmo onse. Popeza kuti Baibulo ndilo linali buku lalikulu loŵerenga m’nyumba, oŵerenga Biblia Pitschna analidziŵa dzina la Mlengi.
Komabe, mibadwo yotsatirapo inataya chikondwerero chawo m’nkhani za m’Baibulo. Ambiri sanasamale kuti adziŵe tanthauzo la liwu lakuti “Iehova,” ngakhale atsogoleri achipembedzo sanayeseyese konse kulifotokoza. Nchifukwa chake, mawu ozokota ameneŵa angokhala zokometsera za nyengo yamakedzana.
M’zaka makumi aposachedwapa kuphunzitsa kwapadera kwakhala kukuchitikanso. Mboni za Yehova zabwera kuchokera kuzidikha, zikumathera matchuthi awo m’zigwa zokongola zimenezi ndi kuyesayesa kuphunzitsa nzika zake ponena za Mulungu amene dzina lake ndi Yehova. Mboni zina zasamukiradi m’deralo kotero kuti zithere nthaŵi yowonjezereka zikumauza anthu za zifuno zabwino koposa za Mlengi kaamba ka dziko lapansi ndi anthu. Motero, mawu ozokota Achiromanshi ameneŵa akukhala ndi tanthauzo latsopano pamene anthu akuphunzira za Mulungu woona, Yehova.
[Zithunzi patsamba 32]
IEHOVA PORTIO MEA: Yehova ndiye gawo langa.—Onani Salmo 119:57