‘Zochita Zake Zimtsata’
PA 8:50 a.m. Lachinayi, July 28, 1994, George D. Gangas anamaliza moyo wake wa padziko lapansi. Iye anali ndi zaka 98 zakubadwa. George Gangas anali mmodzi wa odzozedwa amene anakhala chiŵalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova chiyambire October 15, 1971.
Onse amene anadziŵana ndi Mbale Gangas anadziŵa za kukonda kwake chilungamo ndi kuda choipa. Amakumbukira bwino lomwe mmene ankafotokozera Satana mobwerezabwereza kukhala wabodza wonyansitsa, wonga chinjoka, woipitsitsa, wopanda khalidwe, ndi woluluzika. Mosiyana ndi zimenezo, iye anafotokoza Yehova kukhala Atate wachikondi, wokoma mtima, wachifundo, waukoma, ndi wosamala. Ambiri amakumbukiranso kukonda kwake kufunsa mafunso a Baibulo. Pokambitsirana nkhani iliyonse, iye sankalephera kufunsa mafunso—ena a iwo okhweka, ena a iwo ofuna kulingalira kwambiri. Indedi, iye anakonda choonadi cha Baibulo.
Mbale Gangas anabatizidwa pa July 15, 1921. Anayamba ntchito yake mu utumiki wanthaŵi yonse wa kulalikira (upainiya) mu March 1928. Motero, anakhala muutumiki wanthaŵi yonse zaka 66. Anakhala chiŵalo cha antchito a pamalikulu a Watch Tower Bible and Tract Society ku Brooklyn pa October 31, 1928.
Nkhani ya moyo wake inatuluka m’kope la The Watchtower la October 15, 1966. Imalongosola munthu wauzimu weniweni wa Mulungu. M’nkhani imeneyo, iye ananena mawu otsatiraŵa: “Ndimakonda moyo ndipo ndimafuna kuti abale anga apeze moyo. Mogwirizana ndi mtumwi Paulo, ndimayesa zina zonse kukhala ‘chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Kristu Yesu.’”—Afilipi 3:8.
Mbale Gangas anasonyeza ndi zochita zake kuti, ndithudi, anakonda moyo, ndipo anauza ena za ‘chizindikiritso chake cha Kristu Yesu’ mofunitsitsa. Adzalakalakidwa, komano tili okondwa chotani nanga kuti tsopano iye walandira mphotho yake yakumwamba! Tsopano, ‘adzapuma pantchito yake, pakuti zochita zake zimtsata.’—Chivumbulutso 14:13, New International Version.