Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 2/1 tsamba 8
  • Mbiri Yabwino ya Ufumu Idzalalikidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbiri Yabwino ya Ufumu Idzalalikidwa
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Mbiri Yabwino Imeneyi Iyenera Kulalikidwa Choyamba
    Nsanja ya Olonda—1994
  • ‘Umboni kwa Anthu a Mitundu Yonse’
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kutumikira Mulungu Wodalirika
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Mboni za Yehova
    Kukambitsirana za m’Malemba
Nsanja ya Olonda—1995
w95 2/1 tsamba 8

Olengeza Ufumu Akusimba

Mbiri Yabwino ya Ufumu Idzalalikidwa

KWA zaka mazana ambiri, mdani wamkulu wa Mulungu, Satana Mdyerekezi, wagwiritsira ntchito mwamachenjera maboma andale ndi chipembedzo chonyenga pa kuyesayesa kwake kuletsa kufalikira kwa Chikristu choona. Koma njira zimenezi zidzalephera. Yesu analosera kuti “mbiri yabwino . . . ya ufumu idzalalikidwa [osati kuti, “ingalalikidwe” kapena, “ikhoza kulalikidwa”] pa dziko lonse lapansi lokhalamo anthu kukhala umboni ku mitundu yonse.”​—Mateyu 24:14, NW.

Kulephera kwa Satana kwaonekera m’Greece. M’dzikolo, Tchalitchi cha Greek Orthodox chayesa kuletsa Mboni za Yehova kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu. Koma, monga momwe chochitika chotsatirachi chikusonyezera, ziphunzitso zoona za Baibulo m’kupita kwa nthaŵi zimafikira anthu oona mtima ngakhale pali chitsutso.

Pafupifupi zaka 30 zapitazo, wansembe wa Greek Orthodox analandira mbiri yabwino nasonyezadi chikhumbo cha kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Komabe, achibale ake anamtsutsa mwamphamvu namkakamiza kuleka kugwirizana ndi Mboni. Pofuna kukondweretsa banja lake, iye anapitiriza ndi ntchito yake monga wansembe; komabe, nthaŵi zonse anazindikira kuti Mboni za Yehova zinamthandiza kudziŵa choonadi ndi kuti anachisiya chifukwa cha malo apamwamba m’chipembedzo chonyenga.

Komatu, iye nthaŵi zina anachirikiza Mboni za Yehova mpata utapezeka. Nthaŵi zingapo iye analangizadi anthu kuti ngati anafuna kudziŵa ziphunzitso zoona za Baibulo, anafunikira kuphunzira ndi Mboni. M’zaka zimene zinatsatira, ena anatsatiradi malangizo ake.

Posachedwapa wansembeyo anadwala kwambiri ndipo anadziŵa kuti mwina akafa posapita nthaŵi. Ali m’chipatala, anaitana ana ake, ndipo onsewo anaima m’mbali mwa kama wake.a Ndiyeno anawauza kuti iye akamwalira, iwo angadzaonanenso naye. Anawauza chiphunzitso cha Baibulo chonena za kuukitsidwa kwa anthu ndi Yehova kudzakhala m’paradaiso padziko lapansi, koma ngati iwo akafunadi kuona zimenezo zikuchitika, akafunikira kuphunzira choonadi cha Baibulo ndi kudzilekanitsa ndi chipembedzo chonyenga. Anawadandaulira kuyanjana ndi Mboni za Yehova ndi kuphunzira kwa iwo mmene angakhalire Akristu enieni.

Posapita nthaŵi, wansembeyo anamwalira. Komabe, uphungu wake wotsazikira ana ake unabala zipatso zabwino. Mwana wake wamkazi, mofanana ndi achibale ake ochuluka, anali kutsutsa kwambiri Mboni za Yehova ndi ntchito yawo. Koma analephera kunyalanyaza kuchonderera koona mtima kwa atate wake omwe anali kufa, chotero mosataya nthaŵi anafuna Mboni za Yehova nayamba kuphunzira Baibulo. Posachedwapa mkazi ameneyo anakhala Mboni, akumapatulira moyo wake kwa Yehova Mulungu nasonyeza kudzipatulira kwake mwa ubatizo wa m’madzi.

M’Greece, mofanana ndi m’maiko ena 230, Mboni za Yehova zimadalira mphamvu ya mzimu woyera wa Mulungu. Iwo amakhala ndi phande m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu wotsatirawu mwa chichirikizo chokwana cha mzimu woyera: “Mudzalandira mphamvu, mzimu woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.”​—Machitidwe 1:8.

[Mawu a M’munsi]

a Tchalitchi cha Greek Orthodox chimalola ansembe ake kukwatira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena