“Monga Masiku a Mtengo”
ZOPOSA zaka zikwi zitatu zapitazo, Mose analemba kuti: “Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi aŵiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwawo kumati chivuto ndi chopanda pake.”—Salmo 90:10.
Mosasamala kanthu za kupita patsogolo m’zamankhwala, utali wa moyo wa munthu ukali wofanana ndi mmene unalili m’tsiku la Mose. Komabe, anthu sadzapitirizabe kukhala ndi moyo waufupi wotero. M’buku la Baibulo la Yesaya, Mulungu anati: “Monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo.”—Yesaya 65:22.
Umodzi wa mitengo yokhalako nthaŵi yaitali kumalo kumene Baibulo linalembedwera ndiwo mtengo wa azitona. Mtengo umene wajambulidwa pano uli umodzi wa mitengo yambiri ya azitona yokhalako zaka chikwi imene idakali yambiri mu Galileya. Kodi ndi liti pamene anthu adzakhala ndi moyo wautali chotero? Ulosi umodzimodziwu ukufotokoza kuti ndi pamene Mulungu adzalenga “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.”—Yesaya 65:17.
Buku la Chivumbulutso limaloseranso za kukhazikitsidwa kwa “m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano”—boma latsopano lakumwamba ndi chitaganya cha anthu chatsopano pamene Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.”—Chivumbulutso 21:1, 4.
Lonjezo limeneli la Mulungu lidzakwaniritsidwa posachedwa. Panthaŵiyo, ngakhale masiku a mtengo wa azitona adzangokhala ngati tsiku wamba la maola 24. Ndipo tidzakhala ndi nthaŵi yokwanira ya kusangalala mokwanira ndi ntchito ya manja athu.