Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 3/15 tsamba 3-4
  • Kodi Mungachititse Motani Mapemphero Anu Kukhala Atanthauzo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungachititse Motani Mapemphero Anu Kukhala Atanthauzo?
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Mapemphero Amene Amayankhidwa
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kuphunzira Baibulo Kungathandize Kuti Mapemphero Anu Azikhala Atanthauzo
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Ndimapemphero Ayani Omwe Amayankhidwa?
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 3/15 tsamba 3-4

Kodi Mungachititse Motani Mapemphero Anu Kukhala Atanthauzo?

PEMPHERO nlapadera pakati pa zogaŵira zachikondi za Yehova Mulungu. Otsutsa angakulandeni Baibulo lanu kapena kukuletsani kusonkhana ndi olambira anzanu, koma palibe amene angakulandeni pemphero. Pemphero nlofunika kwambiri. Pamenepa, nkofunika chotani nanga kwa aliyense wa ife kulemekeza ndi kugwiritsira ntchito bwino mwaŵi umenewu. Kodi chimene chingakuthandizeni kuchititsa mapemphero anu kukhala atanthauzo nchiyani?

Baibulo si buku la mapemphero. Komabe, lingafotokozedwe kukhala buku la anthu lokhala ndi zambiri koposa ponena za mapemphero. Malemba Achihebri okha ali ndi mapemphero oposa 150. Ena ndi aafupi; ena ndi aatali. Aperekedwa poyera kapena mseri, ndi mafumu kapena andende, pachilakiko kapena m’nsautso. Monga momwe Davide anaimbira m’Salmo 65:2, “zamoyo zonse” zimatembenukira kwa Yehova, “Wakumva pemphero.” Kodi nchifukwa ninji Mulungu anauzira alembi a Baibulo kulemba mapemphero osiyanasiyana amenewo?

Kuyankha funsolo, onani 2 Timoteo 3:16. Amati: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa.” Motero, mapemphero a m’Baibulo analembedwa kutitsogoza ife, mofanana ndi maulosi a m’Malemba, malamulo, ndi mbiri yake. Kodi mapemphero ameneŵa angatipindulitse motani?

Mwa kusinkhasinkha mapemphero a m’Malemba, tingathe kudziŵa amene anaperekedwa m’mikhalidwe yonga yathu. Tingathe kudziŵa mmene zifuno ndi mkhalidwe wa mapemphero zimasiyanirana. Ndiponso, tidzapeza mawu atsopano a chitamando ndi chiyamiko ndipo tidzapeza mawu abwino a zopempha zathu ndi mapembedzero. Mwachidule, mapemphero a m’Baibulo angatithandize kuchititsa mapemphero athu kukhala atanthauzo.

Mariya, amene anakhala amayi wa Yesu, anali munthu amene mwachionekere anapindula ndi mawu ogwiritsiridwa ntchito m’pemphero lolembedwa m’Baibulo. Anakachezera wachibale wake Elisabeti onse aŵiri atakhala ndi pathupi mothandizidwa ndi Mulungu. Mariya anatamanda ndi kuthokoza Mulungu, ndipo mawu ake ena ngofanana kwambiri ndi amene ali m’pemphero la m’Malemba Achihebri. Nkotheka kuti Mariya anali kudziŵa pemphero limene Hana, amake Samueli mneneri, anapereka. Hana nayenso anakhala ndi pathupi mothandizidwa ndi Mulungu, zaka zoposa 1,000 kumbuyoko. Kodi kungakhale kwakuti Mariya anasinkhasinkha pemphero limenelo chifukwa chakuti linasonyeza malingaliro ake?​—1 Samueli 2:1-10; Luka 1:46-55.

Bwanji nanga za inu? Kodi mungakumbukire pemphero la m’Baibulo limene linaperekedwa m’mikhalidwe yonga yanu? Kupeza, kuŵerenga, ndi kusinkhasinkha mapemphero otero kudzakuthandizani kuwongolera kulankhula kwanu ndi Mulungu. M’nkhani yotsatira, tikupemphani kupenda mapemphero atatu a m’Malemba Oyera. Anaperekedwa m’mikhalidwe yosiyana, mwina mwake yofanana ndi yanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena