Mukuitanidwa Mwachikondi
Imfa ya munthuyo Yesu Kristu imene inachitika zaka zoposa 1,900 zapitazo, inali chochitika chofunika koposa m’mbiri ya anthu. Inatsegula mwaŵi wa chiyembekezo cha kulandira moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso. Paphwando losacholoŵanalo, Yesu anagwiritsira ntchito mkate wopanda chotupitsa ndi vinyo monga zizindikiro za nsembe yake yaumunthu yachikondi. Ndiyeno anauza ophunzira ake: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Luka 22:19) Kodi mudzakumbukira chochitika chofunika chimenechi? Mboni za Yehova zikukuitanani mwachikondi kuti mudzachite nazo pamodzi phwando la Chikumbutso Limeneli. Lidzakhalako dzuŵa litaloŵa pa deti lolingana ndi Nisani 14 pa kalenda ya mwezi ya Baibulo. Mukhoza kufika pa Nyumba Yaufumu yapafupi ndi kwanuko. FunsanI Mboni za Yehova za kwanuko ponena za nthaŵi yeniyeni ndi malo. Deti la phwandolo mu 1995 lidzakhala Lachisanu, April 14.