Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 4/15 tsamba 29
  • “Kugulitsa Mchere” m’Mozambique

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kugulitsa Mchere” m’Mozambique
  • Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1995
w95 4/15 tsamba 29

“Kugulitsa Mchere” m’Mozambique

FRANCISCO COANA, chiŵalo cha komiti ya dziko ya Mozambique, anakhala zaka khumi mu “misasa ya maphunziro.” Iye akusimba zimene zinamchitikira: “Ndinadziŵa kuti muno tikakhalamo nthaŵi yaitali, choncho ndinafunsa woyang’anira dera ngati ndikanapitiriza upainiya wokhazikika. Koma kodi ndikanaipeza motani nthaŵi yokwanira ya utumiki wa poyera, popeza kuti pafupifupi aliyense m’misasayo anali mmodzi wa Mboni za Yehova? Ndinanena kuti ndidzapita ku Milange, tauni yokhala pamtunda wa makilomita 47, kuti ndikapeze anthu olalikirako.

“Ngakhale kuti boma silinali kutilola kuchoka mumsasawo, lamulo limeneli silinali kugwira ntchito kwambiri. Ndikumbukira kuti ndinkapita m’thengo, kugwada, ndi kupemphera za njira yolalikira anthuwo. Posapita nthaŵi Yehova anayankha.

“Ndinakaonana ndi mwamuna wina yemwe anali ndi njinga, ndipo ndinapangana naye. Iye anavomera kuti ngati ndimlimira munda wake wa mahekita 0.75 dzinja lisanafike, akandilipira njinga yakeyo. Chotero masiku onse mmaŵa ndinali kulima m’munda mwake. Yehova anadalitsa makonzedwe ameneŵa, pakuti pomaliza ndinalandira njingayo.

“Chotsatirapo nchakuti ndinakhoza kupita kutauni yaikulu ya Milange ndi kuchita upainiya wanga bwino lomwe m’munda wobala zipatso kwambiri umenewu. Popeza ntchito yathu inali yoletsedwa, ndinakakamizika kupeka njira youzira anthu choonadi. Nditabisa mabuku ndi magazini m’malaya anga, ndinanyamula thumba la mchere ndi kumakagulitsa. M’malo mougulitsa pa 5 meticais, ndimachita 15 meticais. (Ukanakhala wotchipa kwambiri, anthu akanaugula wonse, ndipo ndikanakhala wopanda mchere wina wogwiritsira ntchito polalikira aliyense!) Kukambitsirana kwathu kunali kuyenda motere:

“‘Moni! Lero ndikugulitsa mchere.’

“‘Muchita bwanji?’

“‘15 meticais.’

“‘Iii. Wadula kwambiri!’

“‘Nzoona, ngwoduladi. Koma ngati muganiza kuti wadula lero, ingoyembekezerani, chifukwa posachedwapa udzadula koposa. Kodi mudziŵa kuti zimenezi Baibulo linazineneratu?’

“‘Zimenezo sindinaziŵerengepo m’Baibulo langa.’

“‘Eya zilimodi mmenemo. Bweretsani Baibulo lanu ndikusonyezeni.’

“Motero kukambitsiranako kunkapitiriza tikumagwiritsira ntchito Baibulo lake, kuti langa likhalebe lobisa m’malaya. Ndinali kuwaŵerengera Chivumbulutso chaputala 6, chonena za mikhalidwe yovuta ndi njala. Nditaona kuti akufunitsitsa, ndinali kutulutsa Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya kapena Mbiri Yabwino Yokusangalatsani ndi kuyambitsa phunziro la Baibulo lenileni.

“Choncho ndinakhoza kupanga kagulu ka ofunitsitsa 15 ku Milange. Koma sipanapite nthaŵi kuti akulu a boma adziŵe zimene tinkachita. Tsiku lina pamene ndinali kuchititsa phunziro la Baibulo, apolisi analoŵa mwadzidzidzi natigwira. Ife tonse, ndi ana omwe a m’banjalo, anatipereka kupolisi. Titakhalako mwezi umodzi, tonsefe anatibwezera kumsasa.”

Zochitika zimenezi sizinazime changu cha abale athu. M’malo mwake, Francisco ndi banja lake, limodzi ndi abale awo zikwizikwi amene anali m’misasamo, tsopano ali ndi ufulu wa kulambira ndi kulalikira m’Mozambique.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena