Katswiri Achita Chidwi ndi New World Translation
MALINGA ndi kunena kwa katswiri wa Chigiriki chamakedzana Dr. Rijkel ten Kate, matembenuzidwe a Baibulo Achidatchi samamasulira molondola mawu ena. Mwachitsanzo, mu Luka chaputala 2, timapeza mawu osiyana atatu Achigiriki (breʹphos, pai·diʹon, ndi pais) ogwiritsiridwa ntchito kufotokoza msinkhu wa Yesu panthaŵi zosiyanasiyana. Mawu ameneŵa lililonse lili ndi tanthauzo losiyana. Komabe, m’ma Baibulo ambiri, mawu aŵiri kapena onse atatu amamasuliridwa mwachisawawa kukhala “mwana.” Kodi ndi matembenuzidwe ati amene ali olondola?
Dr. ten Kate akulongosola kuti m’vesi 12 liwu Lachigiriki la breʹphos limatanthauza “mwana wongobadwa kumene, kapena khanda.” Paidiʹon, logwiritsiridwa ntchito m’vesi 27, limatanthauza “kamnyamata kapena kamwana,” ndi pais, lopezeka m’vesi 43, liyenera kumasuliridwa kukhala “mnyamata.” “Malinga ndi zimene ndidziŵa,” analemba motero Dr. ten Kate m’kope la March 1993 la Bijbel en Wetenschap (Baibulo ndi Sayansi), “palibe matembenuzidwe alionse Achidatchi amene amasulira zimenezi molondola, kutanthauza, mogwirizana ndendende ndi malemba oyambirira.”
Pambuyo pake, Dr. ten Kate anasonyezedwa New World Translation of the Holy Scriptures, imene ili m’zinenero 12, kuphatikizapo Chidatchi. Kodi ananenanji? “Ndadabwa kwambiri,” iye anatero, “kuti lilipodi Baibulo Lachidatchi mmene matanthauzo osiyana a mawu atatuwo Achigiriki breʹphos, pai·diʹon, and pais analingaliridwa bwino.” Kodi New World Translation imamasulira mavesi ameneŵa mogwirizana ndi malemba Achigiriki oyambirira? “Imagwirizana nawo ndendende,” anayankha motero Dr. ten Kate.