Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 6/15 tsamba 32
  • Akazi Padziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akazi Padziko Lonse
  • Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1995
w95 6/15 tsamba 32

Akazi Padziko Lonse

PAMENE anthu aŵiri oyamba anapandukira Mulungu, Yehova analosera za zotulukapo zoipa zimene zinali kudzagwera iwo ndi mbadwa zawo zomwe. Yehova anati kwa Hava: “Udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira.” (Genesis 3:16) Baibulo nthaŵi zonse limalimbikitsa kuchitira ulemu waukulu akazi, ndipo akazi ambiri ali ndi moyo wokhutiritsa ndi wachimwemwe kwambiri chifukwa chakuti iwo ndi mabanja awo amagwiritsira ntchito malamulo a Baibulo.

Komabe, malinga ndi lipoti lina laposachedwapa lonena za ufulu wa anthu, akazi ena ambiri padziko lonse amanyazitsidwa, kulimidwa pamsana, ndi kusulizidwa. Pothirira ndemanga pa lipotilo, International Herald Tribune ikuti: “Mwa mafotokozedwe osamalitsa, lipotilo la maiko 193 . . . likupereka chithunzi chomvetsa chisoni cha kupatula akazi tsiku ndi tsiku ndi kuwachitira nkhanza.”

Nazi zitsanzo zoŵerengeka: Pakati pa Afirika, asungwana amachita ntchito yochuluka yovuta ya m’mafamu, ndipo anyamata oŵirikiza katatu kuposa asungwana amapita kusukulu. M’dziko lina kumeneko, chigololo nchololeka kwa amuna koma osati kwa akazi. Lamulo la dziko lina mu Afirika limachotsera mwamuna mlandu ngati wapha mkazi wake atamgwira akuchita chigololo, koma lamulolo silimachotsera mkazi mlandu ngati wapha mwamuna wake m’mikhalidwe yofanana ndi imeneyo.

Lipotilo likunena kuti kumbali zina za South America, apolisi alibe chifundo kwa akazi omenyedwa. Ndipo kaŵirikaŵiri akazi amene amagwira ntchito amalandira malipiro ochepa kuposa aja a amuna ndi 30 kapena 40 peresenti.

Kumbali zina za Asia, akazi amakakamizidwa kutseka matumbo ndi kutaya mimba. M’dziko lina, muli mahule pafupifupi 500,000, amene ambiri a iwo anagulitsidwa ndi makolo awo ofuna ndalama zowathandiza kugulira nyumba zawo zatsopano. Apolisi m’dziko lina akulimbana ndi kufalikira kwa “imfa za malowolo”​—mkazi amaphedwa ndi mwamuna wake kapena achibale a mwamuna chifukwa chakuti malowolo amene mkaziyo analipira anapereŵera.

Ponena za Yesu Kristu, Baibulo limatilonjeza kuti: “Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wamtengo pamaso pake.” (Salmo 72:12-14) Chotero tili ndi chifukwa choyembekezera zabwino; akazi padziko lonse angayembekezere ndi chidwi mikhalidwe yabwino imene idzakhalako nthaŵiyo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena