“Sikungaletsedwe ndi Maganizo Olama”
“POPEZA kuti nkhondo zimayambira m’maganizo mwa anthu, ndi m’maganizo mwa anthu mmene tiyenera kumanga malinga a mtendere.” (Tchata cha UN Educational, Scientific, and Cultural Organization) Akumakumbukira mawu ameneŵa, akatswiri oposa 500 pamsonkhano wa UN wa 1993 wotula zida analingalira za mbali ya chipembedzo pa kumanga malinga otero.
Jonathan Granoff, akumaimira Lawyers’ Alliance for World Security, anatsogolera msonkhanowo. Iye anati: “Kulimbana kwa zipembedzo ndi mafuko komwe kulipo kuli kwakukulu kwakuti sikungaletsedwe ndi khalidwe laulemu, mwinamwake sikungaletsedwe ndi maganizo olama.” Mawu a John Kenneth Galbraith anagwidwa moyenerera pamsonkhanowo: “Anthu ambiri aphedwa m’dzina la chipembedzo kuposa m’nkhondo zonse ndi masoka achilengedwe kuziika pamodzi.”
Dr. Seshagiri Rao anati: “Madokotala afunikira kuchiritsa matenda osati kuwawanditsa. Miyambo yachipembedzo siyenera kufalitsa udani ndi kulimbana kwachiwawa pakati pawo. Iyo iyenera kukhala mphamvu yoyanjanitsa. Komabe kwenikweni, iyo kaŵirikaŵiri yagwira ntchito ndipo ikali kugwira ntchito monga mphamvu yogaŵanitsa.”
Zaka zingapo zapitazo, Catholic Herald ya ku London inanena kuti mtendere ungapezeke “ngati matchalitchi a lerolino mogwirizana angatsutse nkhondo.” Komabe, nyuzipepalayo inawonjezera kuti: “Tikudziŵa kuti zimenezi sizidzachitika.” Panthaŵi ina mvirigo wina Wachikatolika ananena kuti: “Dziko lingakhale losiyana chotani nanga ngati kuti mmaŵa wina tidzuka ndi kutsimikiza mtima zolimba kusanyamulanso zida, . . . mofanana ndi Mboni za Yehova!”
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Tom Haley/Sipa Press