Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 8/15 tsamba 32
  • Chimasuko kwa Operekedwa Nsembe Osadziŵa Kanthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chimasuko kwa Operekedwa Nsembe Osadziŵa Kanthu
  • Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1995
w95 8/15 tsamba 32

Chimasuko kwa Operekedwa Nsembe Osadziŵa Kanthu

KUPEREKA ana nsembe kwa chipembedzo kuli pakati pa maupandu oipitsitsa amene munthu wachita. Ena sakhulupirira kuti mchitidwe wonyansitsa umenewo unachitika. Koma mbali imeneyi ya kulambira kwa Afoinike yatsimikizidwa ndi zopeza zambiri za ofukula m’mabwinja.

Ana a m’mabanja apamwamba anaperekedwa nsembe m’moto kwa milungu yonga Tanit ndi Baal-Hammon. Ku Carthage ana anawatentha monga nsembe kwa fano lachitsulo la Kronos. Diodorus Siculus, wolemba mbiri wa m’zaka za zana loyamba B.C.E., akuti achibale a mwana sanali kuloledwa kulira. Mwinamwake anakhulupirira kuti misozi yachisoni ikanasukuluza mtengo wa nsembeyo.

Kwa nthaŵi yaitali dzoma longa limenelo linkachitika pafupi ndi Yerusalemu ku Tofeti wakale. Kumeneko alambiri ankavina ndi kuliza malingaka kuti asamve kulira kwa mwana pamene anaponyedwa m’ng’anjo ya moto m’mimba mwa Moleke.​—Yeremiya 7:31.

Yehova amakwiya nawo kwambiri aja amene mokakala mtima amatseka makutu awo kuti asamve za zopweteka za ena. (Yerekezerani ndi Miyambo 21:13.) Pokhala Mulungu wachifundo kwa ana, Yehova adzaphatikizadi operekedwa nsembewo osadziŵa kanthu pa “kuuka kwa olungama ndi osalungama.”​—Machitidwe 24:15; Eksodo 22:22-24.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena