Mwambo Wopanda Tanthauzo?
SAKARAMENTI ya kuulula machimo yachitidwa ndi Akatolika kwa zaka mazana ambiri. Komabe, kwa ambiri yakhala chizoloŵezi chopanda ntchito. Pofotokoza za ubwana wake, mphunzitsi wamkulu wina wa kusekondale wotchedwa Bob akuti: “Ndinali wachichepere, ndipo ngakhale panthaŵiyo sindinakuone monga nkhani yaikulu.” Chifukwa ninji? Kwa iye, kuulula machimo kunakhala mwambo wopanda tanthauzo. Akufotokoza kuti: “Kuulula machimo kunali ngati kubweretsa katundu wako wodzala ndi machimo kwa munthu wa kasitomu pa bwalo la ndege. Munthuyo akukufunsa mafunso onena za machimo ako ndiyeno akukulola kupyola utalipira msonkho wa zinthu zokwera mtengo zimene unagula pamene unali kunja.”
Mofananamo, Frank Wessling, polemba mu U.S. Catholic, akufotokoza mchitidwe wa kuulula machimo kukhala “chitsogozo chofeŵetsedwa kwambiri cha kulondola masitepe ake, kuyambira pa kuchotsa machimo wamba kupyolera m’pemphero loloŵezedwa pamtima la kuulula machimo kufikira ku mchitidwe wamwambo wa sakaramenti.” Kodi kugamula kwa Wessling nkotani? “Ndili wokhutira kuti Kuulula Machimo nkwabwino kwa munthu,” iye akutero. “Koma mmene Akatolika amakuchitira kuli vuto.”
Baibulo limafotokoza kuulula machimo m’njira yosiyana kwambiri. Kuulula machimo kofunika koposa ndiko kochitidwa kwa Mulungu. (Salmo 32:1-5) Ndipo wophunzira Wachikristu Yakobo analemba kuti: “Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la [Yehova, NW]. Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe.”—Yakobo 5:14, 16.
Mkristu wolemetsedwa ndi tchimo angafikire oyang’anira a mumpingo, amene amapereka mwachindunji uphungu wabwino wa m’Baibulo wa kuthandiza wochita cholakwayo kuti asiye njira yake yauchimo. Oyang’anira angapereke chilimbikitso choyenera pamene ayang’anira kuwongokera kwa munthu amene akudwala mwauzimu. Zimenezi nzosiyana chotani nanga ndi mchitidwe wamwambo wa kuulula machimo wochitidwa ndi matchalitchi lerolino! Pokhala atalimbitsidwa ndi thandizo laumwini la akulu a mumpingo, ochita cholakwa olapa amapeza mpumulo umene Davide anali nawo, monga momwe anafotokozera m’salmo lina kuti: “Ndinavomera choipa changa kwa inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.”—Salmo 32:5.