Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 11/1 tsamba 32
  • ‘Monga Chitsulo Chinola Chitsulo’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Monga Chitsulo Chinola Chitsulo’
  • Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1995
w95 11/1 tsamba 32

‘Monga Chitsulo Chinola Chitsulo’

CHAKUMAPETO kwa zaka za zana lachitatu C.E., mwamuna wina woona mtima wotchedwa Anthony, wonenedwa kukhala “Mkristu Wachikoputi,” anachoka pakati pa anthu ndi kukakhala yekha zaka 20 m’chipululu. Chifukwa ninji? Anaganiza kuti iyi ndiyo inali njira yabwino koposa yoti atumikiriremo Mulungu. Anali wodzipatutsa woyamba wachisonkhezero chachikulu wa Dziko Lachikristu.

Lerolino, Dziko Lachikristu lili ndi odzipatutsa angapo. Koma anthu omawonjezereka akufuna kudzipatutsa m’njira ina yake. Iwo amakana kulankhulana ndi ena ponena za chipembedzo, akumalingalira kuti nkhani zotere zimachititsa mikangano ndi ndewu. Kulambira kwawo kwenikweni ndiko kwa kusavulaza mnansi.

Zoonadi, kusavulaza mnansi kuli mbali ina ya chipembedzo choona, koma zambiri zimafunika. Mwambi wakale umati: “Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.” (Miyambo 27:17) Choonadi ndicho chakuti, Baibulo limalimbikitsa Akristu kukumana pamodzi, osati kudzipatutsa kotheratu kudziko kapena kwa Akristu ena. Ilo limati: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi.” (Ahebri 10:24, 25) Mboni za Yehova zimatsatira uphungu umenewo. Nthaŵi zoŵirikiza pa mlungu, amakumana pamodzi ‘kunolana nkhope,’ kumangirira chikhulupiriro cha okhulupirira anzawo. Iwo amaona kuti kukambitsirana za m’Baibulo moona mtima sikumachititsa ndewu. M’malo mwake, kumachititsa chigwirizano ndi mtendere. Kuli mbali yofunika koposa ya kulambira koona.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena