Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 11/15 tsamba 20
  • Milungu Yachikazi ya Kubala ndi ya Nkhondo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Milungu Yachikazi ya Kubala ndi ya Nkhondo
  • Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1995
w95 11/15 tsamba 20

Milungu Yachikazi ya Kubala ndi ya Nkhondo

PANTCHITO ya kufukula za m’mabwinja ku Ebla, Syria, chifanizo chosonyeza Ishtar, mulungu wachikazi wa Chibabulo wa kubala ndi wa nkhondo, chinapezedwa. Katswiri wa za m’mabwinja Paolo Matthiae akuchifotokoza kukhala “chizindikiro chachitali chokhala ndi chithunzithunzi cha kulambira chosonyeza wansembe wachikazi wophimba kumaso ataimirira patsogolo pa fano limodzi la mulungu . . . ndi mutu wake womamatira ku mzati wautali.”

Chopezekacho nchapadera, popeza fanolo nlakuchiyambi kwa zaka za zana la 18 B.C.E. Malinga ndi Matthiae, chimenechi chimapereka “umboni wotsimikiza” wakuti kulambira Ishtar kunakhalapo kwa zaka 2,000.

Kulambira Ishtar kunayamba mu Babulo ndipo m’zaka mazana zotsatirapo kunafala mu Ufumu wonse wa Roma. Yehova analamula Aisrayeli kuchotsa kanthu kalikonse ka chipembedzo chonyenga m’Dziko Lolonjezedwa, koma popeza analephera kuchita motero, kulambira kwa Astaroti (mulungu wa Chikanani mnzake wa Ishtar) kunakhala msampha kwa iwo.​—Deuteronomo 7:2, 5; Oweruza 10:6.

Ngakhale kuti Ishtar ndi mnzake Astaroti saliponso, makhalidwe amene anaimira​—chisembwere ndi chiwawa​—nzofala. Tingafunse kaya chitaganya chamakono chiridi chosiyana kwambiri ndi anthu akale amenewo amene analambira milungu yachikazi imeneyi ya kubala ndi ya nkhondo.

[Chithunzi patsamba 20]

Ana anaperekedwanso nsembe kwa Tanit

[Mawu a Chithunzi]

Ralph Crane/​Bardo Museum

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena