Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 11/15 tsamba 31
  • ‘Musakhale Omangidwa m’Goli Losiyana’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Musakhale Omangidwa m’Goli Losiyana’
  • Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1995
w95 11/15 tsamba 31

‘Musakhale Omangidwa m’Goli Losiyana’

NG’OMBE ziŵirizi zosonyezedwa pano zili ndi mphamvu yaikulu, yozichititsa kukoka zinthu zolema mosavuta. Koma bwanji ngati ng’ombe imodzi ichotsedwapo ndi kuikapo bulu. Popeza bulu ali wamng’onopo ndi wochepa mphamvu kuposa ng’ombe, mwachionekere angakane mwa kumenya goli losiyanalo. Motero, chifukwa cha chimenechi, lamulo la Mulungu kwa Aisrayeli linati: “Musamalima ndi bulu ndi ng’ombe zikoke pamodzi.”​—Deuteronomo 22:10.

Mtumwi Paulo analemba zonga zimenezi ponena za anthu. Iye anati: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana.” (2 Akorinto 6:14) Muyenera kukumbukira zimenezi makamaka posankha mnzanu wa mu ukwati. Ukwati uli chigwirizano chachikhalire, pakuti Yesu Kristu anati: “Chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mateyu 19:6) Kupsinjika kwakukulu kumakhalapo pamene okwatirana sagwirizana pa zikhulupiriro zawo, miyezo, ndi zonulirapo. Motero kulidi kwanzeru kulondola uphungu wa Baibulo wa kukwatira “kokha mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39, NW) Kuloŵa mu ukwati ndi munthu amene sagwirizana ndi chikhulupiriro chanu cha chipembedzo kungachititse vuto lalikulu kuposa kumanga ng’ombe ndi bulu m’goli.

Kusiyana kwa zikhulupiriro za chipembedzo kuli chabe mbali imodzi imene ingachititse okwatirana kumangika m’goli losiyana. Oyandikira kuloŵa mu ukwati​—ngakhale a chikhulupiriro chimodzi​—angachite bwino kufunsa kuti, ‘Kodi tili ndi zonulirapo zofanana? Kodi tidzakhala kuti? Kodi ndani adzayang’anira ndalama? Kodi tonse aŵirife tidzaloŵa ntchito? Nanga bwanji ponena za ana? Kodi chifundo ndi kuganizirana zidzatsogoza unansiwu?’

Pamlingo wina wake, mkhalidwe wa makambitsirano a nkhanizi ukhoza kusonyeza ngati goli lidzakhala lolingana kapena losiyana. Zoona, palibe anthu aŵiri oyenerana m’kalikonse. Komabe, mwachisawawa, ngati aŵiri otomerana angayang’anizane ndi mavuto ndi kuwathetsa pamodzi ndipo ngati angazilankhulana wina ndi mnzake momasuka, kuli kotheka kuti sadzamangidwa m’goli losiyana.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena