Musasunge cha Kukhosi
KUPEŴA mkwiyo kungaoneke kukhala kovuta kwambiri kwa ife pamene wina watiputa. Baibulo lili ndi uphungu wothandiza m’mikhalidwe yotero. “Kwiyani,” analemba motero mtumwi Paulo, “koma musachimwe; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire.”—Aefeso 4:26.
Pamene wina watilakwira, nkwachibadwa kukwiya pamlingo wakutiwakuti. Kunena kwa Paulo kuti “kwiyani” kumasonyeza kuti nthaŵi zina mkwiyowo ungakhale woyenera—mwinamwake chifukwa chochitidwa mosayenera kapena mosalungama. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 11:29.) Koma utalekereredwa, ngakhale mkwiyo woyenera ungakhale ndi zotulukapo zowononga, ukumachititsa tchimo lalikulu. (Genesis 34:1-31; 49:5-7; Salmo 106:32, 33) Choncho, kodi mungachitenji pamene wina wakukwiyitsani?
Pankhani zambiri zokhudza zophophonya zazing’ono, mwina mungaitsirizire mumtima mwanu nkhaniyo ‘ndi kukhala chete’ kapena mungapite kwa wokulakwiraniyo ndi kukambirana nkhaniyo. (Salmo 4:4; Mateyu 5:23, 24) Panjira zonsezo, ndi bwino kuithetsa msanga nkhaniyo kuti mkwiyo usakule ndi kubala zipatso zoipa.—Aefeso 4:31.
Yehova amatikhululukira machimo athu kwaulere ngakhale machimo amene sitingadziŵe kuti tawachita. Kodi nafenso sitingakhululukire zophophonya zazing’ono za munthu mnzathu?—Akolose 3:13; 1 Petro 4:8.
Chokondweretsa nchakuti liwu la Chigiriki la “kukhululukira” kwenikweni limatanthauza “kuleka.” Kukhululukira sikumafuna kuti tichepetse kapena kulekerera choipacho. Nthaŵi zina kungangophatikizapo ‘kuuleka’ mkhalidwewo, pozindikira kuti kusunga cha kukhosi kudzangowonjezera mtolo wanu ndi kusokoneza umodzi wa mpingo Wachikristu. Ndiponso, kusunga cha kukhosi kungawononge thanzi lanu!—Salmo 103:9.