Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 1/1 tsamba 2-4
  • Kodi Mtendere Ngwotheka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mtendere Ngwotheka?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Angaichititse Ndani?
    Galamukani!—2004
  • Kuopa Nyukiliya—Sikunathe Ngakhale Pang’ono
    Galamukani!—1999
  • Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Anthu Akuiopabe?
    Galamukani!—2004
  • Potsiriza Pake Tsogolo Lopanda Choopsa!
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 1/1 tsamba 2-4

Kodi Mtendere Ngwotheka?

“NTHAŴI zonse kudzakhalabe nkhondo kwinakwake. Chimenecho ndi choonadi chomvetsa chisoni ponena za anthu.” Lingaliro limeneli losayembekezera zabwino linatuluka posachedwapa m’kalata yochokera kwa woŵerenga m’magazini a Newsweek. Kodi mukulivomereza? Kodi nkhondo njosapeŵeka ndiponso mtendere ngwosatheka? Ngati tipenda nkhaniyi ndi zochitika za m’mbiri, timakakamizika kuyankha kuti inde pamafunso aŵiriŵa. Malinga ndi mbiri, anthu achita nkhondo zotsatizanatsatizana, ndipo nkhondozo zinakhala zowononga kwambiri pamene anthu anapanga njira zowopsa zopherana.

Zakhalanso choncho m’zaka za zana la 20. Ndithudi, mwachitika nkhondo zokhetsa mwazi kowopsa zimene sizinachitikepo, koma mwachitikanso kanthu kena katsopano. Zaka 50 zapitazo United States anayamba nyengo ya nyukiliya mwa kuponya mabomba aŵiri aatomu pa Japan. Pazaka makumi asanu chiyambire pamenepo, mitundu yakundika nkhokwe zazikulu za zida zanyukiliya zimene zingawononge anthu onse kuŵirikiza nthaŵi zambiri. Kodi kukhalako kwa zida zanyukiliya kudzawopseza anthu potsirizira pake kuti aleke kuchita nkhondo? Maumboni akudzilankhulira okha. Chiyambire 1945 anthu mamiliyoni ambiri afa m’nkhondo​—ngakhale kuti pakali pano palibe mabomba ena anyukiliya amene aponyedwa.

Kodi nchifukwa ninji anthu amakonda nkhondo? Encyclopedia Americana imatchula mbali zina za umunthu zimene malinga ndi mbiri zachititsa nkhondo. Zimaphatikizapo kusalekererana kwa zipembedzo, kusankhana mafuko, kusiyana miyambo, ziphunzitso zosiyana (monga Chikomyunizimu ndi chikapitolizimu), utundu ndi chiphunzitso cha ufulu wa kudzilamulira, mikhalidwe ya chuma, ndi kukonda zida zankhondo. Mukaŵerenga mpambo umenewo, kodi mukuona chilichonse chimene mwina chidzasintha patsogolopa? Kodi mitundu idzachepetsako kufunitsitsa kwawo ufulu wa kudzilamulira? Kodi anthu adzachepetsako ufuko? Kodi anthu otengeka maganizo ndi chipembedzo adzachepetsako kutengeka kwawoko? Zimenezi nzosatheka.

Kodi ndiye kuti palibe chiyembekezo chakuti tsiku lina zinthu zidzakhala bwino ndi kuti padzakhala mtendere wachikhalire? Ayi, chiyembekezo chilipo. Mosasamala kanthu za chipwirikiti cha dzikoli, kuli kotheka ngakhale lero kupeza mtendere. Mamiliyoni ambiri aupeza. Taimani kaye tikusimbireni za anthu angapo ameneŵa ndipo onani zimene zowachitikira zawo zingatanthauze kwa inu.

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

Kuchikuto ndi patsamba 32: Reuters/​Bettmann

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Reuters/​Bettmann

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena