“Mufunikira Chipiriro”
‘TIFUNIKIRA chipiriro,’ ngati titi tione ‘kukwaniritsidwa kwa lonjezo.’ (Ahebri 10:36, NW) Katswiri wina wa Baibulo William Barclay akufotokoza kuti liwu lachigiriki lotanthauza “chipiriro” limene mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito m’mawuŵa nthaŵi zina linagwiritsiridwa ntchito kufotokoza “kukhoza kwa chomera kukhalabe ndi moyo pansi pa mikhalidwe yovuta ndi yolimba.”
M’mapiri a ku Ulaya, mumamera chomera chotero. Modabwitsadi, chimatchedwa kuti live-forever (kukhala ndi moyo kosatha). Komabe, chomera cha m’mapiri aatali chimenechi sichimakhala ndi moyo kosatha, koma chimakhalako chaka ndi chaka, chikumatulutsa maluŵa okongola dzinja lililonse. The New Encyclopædia Britannica ikufotokoza kuti dzinalo kukhala ndi moyo kosatha linapatsidwa ku chomeracho chifukwa cha “kulimba [kwake] ndi kukhalitsa.” (Dzina lasayansi la zomera zamtundu umenewu lakuti Sempervivum limatanthauzanso “kukhala-ndi-moyo-kosatha.”)
Chimene chimachititsa chomera chimenechi kukhala chapadera ndicho chakuti chimamera m’malo oipa kwambiri. Chingapezedwe m’mapiri pamwamba mzigwa zokunthidwa ndi mphepo, mmene tempichala ingatsike mofulumira kufika pa 35° C m’maola 24 okha. Chingazike mizu mumng’alu wa mwala mongokhala dothi lochepa. Kodi zinsinsi zake zina zachipiriro chake m’mikhalidwe yoipa motere ndi ziti?
Chomera cha kukhala ndi moyo kosatha chili ndi masamba ochindikala, amene amasunga madzi bwinobwino. Zimenezi zimachikhozetsa kugwiritsira ntchito m’nyontho wonse umene ulipo wochokera kumvula kapena ku chipale chomasungunuka. Ndiponso, chimamera m’masadzi amene amagwirizanitsa nyonga yawo kuti zilimbe pamwala wozichirikizawo. Mwa kuzika mizu m’ming’alu, chimakhala ndi chitetezo china ku machedwe oipa, ngakhale kuti pangakhale dothi lochepa kwambiri. M’mawu ena, chimakhala bwino mwa kugwiritsira ntchito mikhalidwe yovutayo m’njira yabwino koposa.
Kunena mwauzimu, tingadzipeze m’mikhalidwe imene imayesa mkhalidwe wa chipiriro chathu. Kodi nchiyani chidzatithandiza kupirira pansi pa chiyeso? Monga chomera cha kukhala ndi moyo kosatha, tingasunge madzi opatsa moyo a Mawu a Mulungu ndi kuyanjana mwathithithi ndi Akristu oona kaamba ka chichirikizo ndi chitetezo. Koposa zonse, monga duŵalo la ku mapiri aatali tiyenera kumamatira mosatopa ku “thanthwe” lathu, Yehova, limodzinso ndi ku Mawu ake ndi gulu lake.—2 Samueli 22:3.
Zoonadi, chomera cha kukhala ndi moyo kosatha chili chikumbutso chabwino kwambiri chakuti, ngakhale m’mikhalidwe yoipa, tingapirire ngati tigwiritsira ntchito makonzedwe amene alipo. Yehova akutitsimikizira kuti chipiriro chotero chidzatitsogolera ku ‘kuloŵa malonjezano,’ amene kwenikweni adzatanthauza kukhala ndi moyo kosatha.—Ahebri 6:12: Mateyu 25:46.