Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 7/1 tsamba 32
  • Woweruza Milandu Wakale Apepesa—Pambuyo pa Zaka 45

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Woweruza Milandu Wakale Apepesa—Pambuyo pa Zaka 45
  • Nsanja ya Olonda—1996
Nsanja ya Olonda—1996
w96 7/1 tsamba 32

Woweruza Milandu Wakale Apepesa​—Pambuyo pa Zaka 45

M’KHOTI ku Berlin, mu August 1995, woweruza milandu wa m’Bwalo Lalikulu wina wakale anasonyeza kwa mmodzi wa Mboni za Yehova kuipidwa kwake kaamba ka kulakwa kumene anachita zaka 45 zapitazo.

Mu October 1950, Bwalo Lalikulu la German Democratic Republic (GDR) linapatsa Mboni za Yehova zisanu ndi zinayi mlandu wa kuukira boma ndi kuchita ukapirikoni. Aŵiri anaweruzidwira kundende ya moyo wawo wonse, ndipo asanu ndi aŵiri enawo​—kuphatikizapo Lothar Hörnig wazaka 22, woimbidwa mlandu wachinayi kuchokera ku dzanja lamanja pachithunzi​—anaweruzidwa kumangidwa kwanthaŵi yaitali m’ndende.

Zaka makumi anayi pambuyo pake, GDR inakhala mbali ya Federal Republic of Germany. Kuyambira nthaŵi imeneyo akuluakulu akhala akufufuza zina za zisalungamo zimene zinachitidwa mu GDR wakale ndipo ayesa kuweruza awo amene anazichita. Chimodzi cha zisalungamo zotero chinali kuimba mlandu Mbonizo kwa Bwalo Lapamwamba mu 1950.

A.T. , wazaka 80 tsopano, anali mmodzi wa oweruza atatu amene anapereka chiweruzo pamene anaimba mlandu Mboni zisanu ndi zinayizo. Tsopano pokhala atapatsidwa mlandu wa kukhotetsa chiweruzo, anaonekera ku Regional Court ku Berlin kukafotokoza chiweruzo chake.

M’mawu ake ku bwalolo, woweruza wakaleyo anavomera kuti zaka 45 zapitazo anavotera kuti anthuwo anali ndi mlandu, ngakhale kuti anakhalira mbali zilango zazing’onopo. Koma kuimbidwa mlanduko kunamchititsa kuganizaponso. Chifukwa ninji? Mboni za Yehova zinazunzidwa ndi Anazi m’nkhondo yachiŵiri yadziko chifukwa chakuti zinakana kuchirikiza Hitler. Pambuyo pa nkhondo Mboni zinazunzidwanso ndi boma lachikomyunizimu tsopano. Zimenezi zachititsa woweruzayo kukhala “wopsinjika mtima kwambiri.”

Lothar Hörnig anauza bwalolo kuti anatha zaka zisanu ndi theka ali kwayekha ndipo sanamasulidwe m’ndende ya Brandenburg mpaka 1959. Atamva mawu a Hörnig, woweruza wakaleyo analira. “Ndili wachisoni kwambiri,” anatero akusisima. “Chonde ndikhululukire.” Hörnig anavomereza kupepesako.​—Yerekezerani ndi Luka 23:34.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Neue Berliner Illustrierte

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena