Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 8/1 tsamba 32
  • “Kodi Ine Ndikulota?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kodi Ine Ndikulota?”
  • Nsanja ya Olonda—1996
Nsanja ya Olonda—1996
w96 8/1 tsamba 32

“Kodi Ine Ndikulota?”

Lipotili likuchokera ku Malaŵi ndipo likunena za umodzi wa Misonkhano Yachigawo ya “Atamandi Achimwemwe” yopanga mbiri ya Mboni za Yehova yochitika m’chilimwe cha 1995.

“M’MBALI mwa msewu waukulu, chapakati pa mtunda wofika ku gombe lakumadzulo kwa Lake Malaŵi, pali chikwangwani choikidwa kwa nthaŵi yoyamba pambuyo pa zaka 29. Icho chikunena kuti, ‘Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova.’

“Lole yaikulu yaimirira pafupi ndi chikwangwanicho, ndipo mukutsika nthumwi zoposa 200 zochokera ku mzinda wa Mzuzu. Iwo abwera ndi zovala, mabulangete, miphika, zitini, zakudya, nkhuni, ndi mabaibulo kudzatsagana ndi abale ndi alongo awo pafupifupi 3,000 ochokera kumalo ena.

“Pamene tikuwapatsa moni potsika m’lolemo, a George Chikako, azaka 63, afika, akukankha njinga yawo mumchenga, ataitchova kwa masiku aŵiri kuchokera ku Nkhotakota. Kwa zaka zambiri, Mbale Chikako analoŵa m’ndende kanayi konse chifukwa chokana kugonja pa mapulinsipulo a Baibulo. Mbale wake anamwalira chifukwa cha kumenyedwa m’ndende. ‘Kodi Ine Ndikulota?’ akufunsa motero Mbale Chikako. ‘Msonkhanowu ukuchitika masana, ndipo anthuŵa akuimba mofuula nyimbo za Ufumu! Kwa zaka zambiri takhala tikusonkhana mumdima usiku, kuimba monong’oneza nyimbo za Ufumu, ndipo tinkawombera m’manja mwa kusisita manja. Tsopano tikusonkhana poyera, ndipo anthu akudabwa kuona kuti tili ochuluka kwambiri chifukwa amaganiza kuti tili oŵerengeka chabe!’

“Malo osonkhanira achingidwa ndi mpanda wa udzu ndi kufoleredwa ndi mabango kuti pakhale mthunzi. Timisasa tating’ono ndi yaikulu yogonamo nthumwi inamangidwa. Usiku pangomveka mang’ombe okongola a kuimba kosawopa chizunzo.

“Nkoyenera chotani nanga kuti mutu wa msonkhano umati ‘Atamandi Achimwemwe’!”

[Mawu a Chithunzi]

Mountain High Maps® Copyright © 1995 Digital Wisdom, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena