Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 8/1 tsamba 9
  • ‘Khomo Lalikulu la ku Ntchito Latseguka’ ku Cuba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Khomo Lalikulu la ku Ntchito Latseguka’ ku Cuba
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Mbiri Yateokrase
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Nsanja ya Olonda—1996
w96 8/1 tsamba 9

Olengeza Ufumu Akusimba

‘Khomo Lalikulu la ku Ntchito Latseguka’ ku Cuba

MTUMWI Paulo anali mlaliki wapadera wa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Anagwiritsira ntchito mpata uliwonse kuuza ena malonjezo a Mlengi a moyo wamuyaya kwa anthu omvera. Pamene anali kuchezera Efeso wakale, Paulo anaona mkhalidwe wina watsopano umene unamlola kuthandiza anthu owonjezereka. Iye anati: “Ndidzakhala ku Efeso . . . . Pakuti panditsegukira pakhomo lalikulu [la ku ntchito, NW].”​—1 Akorinto 16:8, 9.

Mboni za Yehova ku Cuba nazonso zili mumkhalidwe watsopano. Ngakhale kuti sizinalembetsedwe mwalamulo, Mboni tsopano zitha kuuza anzawo a m’dzikolo chiyembekezo chawo cha m’Baibulo poyera. Posachedwapa boma la Cuba linasonyeza kufunitsitsa kwakukulu kwa kulola magulu achipembedzo osiyanasiyana kugwira ntchito mwaufulu. Pulezidenti Castro watchula Mboni za Yehova poyera monga gulu lachipembedzo limene tsopano lili pa unansi wabwino ndi boma la Cuba.

Mkhalidwe watsopano umenewu watsegula “khomo lalikulu la ku ntchito” kwa Mboni. Mwachitsanzo, posachedwapa Mboni za Yehova zinatsegula ofesi ku Cuba, imene imawathandiza kugwirizanitsa ntchito yawo yolalikira m’dzikomo. Mboni zoposa 65,000 zikuthandiza anthu kuphunzira ndi kumvetsetsa Baibulo. Zimagwiritsira ntchito mabuku ofotokoza Baibulo, monga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Akyuba ambiri okonda chilungamo akupindula ndi kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.

Mboni zikuchitanso misonkhano mokhazikika m’timagulu pachisumbu chonsecho. Nthaŵi zina amakhala ndi mwaŵi ngakhale wa kukhala ndi misonkhano yaikulu m’magulu a anthu pafupifupi 150. Iwo akuyamikiradi chilolezo chimene alandira kuchokera kwa akuluakulu a boma la Cuba, chimene chimawapatsa mpata wa kusonkhana ndi abale ndi alongo awo auzimu, kuimba zitamando kwa Mulungu, ndi kupemphera pamodzi.

Posachedwapa Msonkhano Wachigawo wa “Mantha Aumulungu” unachitidwa nthaŵi zoposa 1,000 mkati mwa masiku a kutha kwa mlungu a milungu itatu yokha. Lipoti lina likunena kuti “dongosolo, kudzisungira, ndi mtendere” zinali kuonekera pa msonkhano wachigawo uliwonse. Akuluakulu anayamikira Mboni pankhaniyi.

Padziko lonse, Akristu enieni amayesetsa kukwaniritsa lamulo lawo loperekedwa ndi Mulungu la kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Panthaŵi imodzimodziyo, amayesetsa kusunga unasi wamtendere ndi akuluakulu a boma. (Tito 3:1) Mboni za Yehova zimatsatira uphungu wa mtumwi Paulo, amene analemba kuti: “Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse; chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m’moyo mwathu tikhale odikha mtima ndi achete m’kulemekezeka Mulungu, ndi m’kulemekeza monse.”​—1 Timoteo 2:1, 2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena