Nthano ya Chigumula Imachirikiza Mbiri ya Baibulo
CHIGUMULA cha dziko lonse cha m’tsiku la Nowa chinachitikadi m’mbiri. Masimbidwe ake amapezeka m’nthano za mafuko ambiri osiyanasiyana kuzungulira dziko lonse. M’dziko la mu Afirika la Chad, fuko la Moussaye limafotokoza Chigumula motere:
‘Kalekale, kumalo akutali kwambiri, kunali banja lina. Tsiku lina, mayi wa banja limenelo anafuna kukonzera okondedwa ake chakudya chokoma. Chotero anatenga mtondo wake ndi munsi kuti asinje ufa wamapira. Panthaŵiyo thambo linali pafupi kwambiri kuposa pamene lili tsopano. Ndipotu, mukanati munyanyamphire mutatukula mkono, mukanalikhudza. Anasinja mapira ndi mphamvu zake zonse, ndipo mwamsanga mapira amene anasinjawo anakhala ufa. Koma posinja paja, mkaziyo mosasamala ananyamula munsiwo kwambiri, naboola thambo! Pomwepo, madzi ochuluka anayamba kugwera padziko lapansi. Imeneyi sinali mvula wamba. Inagwa masiku asanu ndi aŵiri usana ndi usiku kufikira dziko lonse lapansi linamizidwa ndi madzi. Pomagwa mvula ija, thambo linayamba kukwera kufikira pamene lili tsopano—posafikika. Linali tsoka lotani nanga kwa anthu! Chiyambire nthaŵiyo, tinataya mwaŵi wa kukhudza thambo ndi manja athu.’
Chokondweretsa nchakuti nthano zakale zosimba za chigumula cha dziko lonse zimapezeka kuzungulira dziko lonse. Mafuko a eni dziko la America limodzinso ndi Aaborijini a ku Australia onsewo ali ndi nthano zake. Mafotokozedwe ake amasiyanasiyana, koma nthano zochuluka zili ndi lingaliro lakuti dziko lapansi linamizidwa ndi madzi ndi kuti anthu oŵerengeka okha ndiwo anapulumuka m’chombo chopangidwa ndi munthu. Kufala kwa nkhani imeneyi kumachirikizanso mfundo yakuti Chigumula cha dziko lonse chinachitikadi, monga momwe Baibulo limasimbira.—Genesis 7:11-20.