Kukwaniritsidwa kwa Ulosi wa Baibulo
MU Imperial War Museum ku London, England, muli koloko yapadera ndi makina amagetsi otenga chiŵerengero. Pamene kolokoyo ikuyenda, makina otenga chiŵerengero amalira kuti keche pa masekondi 3.31 alionse. Pakulira kulikonse nambala ina imawonjezedwa pa chiwonkhetso. Kulira kulikonse, nambala iliyonse, imaimira mwamuna, mkazi, kapena mwana amene wafa chifukwa cha nkhondo m’zaka za zana lino.
Makinawo anayamba kuŵerengera m’June 1989 ndipo akuyembekezeredwa kumaliza kuŵerengera kumeneko pakati pa usiku wotsatizana ndi chaka cha 2000. Panthaŵiyo chiŵerengero chosonyezedwa pa makinawo chidzakhala mamiliyoni zana limodzi—chiŵerengero choyerekezera cha imfa zochitika chifukwa cha nkhondo m’zaka za zana la 20 lonse.
Pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, Yesu Kristu analosera za nthaŵi pamene kudzakhala ‘kuukirana kwa mtundu pa mtundu wina ndi ufumu pa ufumu wina.’ Mogwirizana ndi zimenezo, Mboni za Yehova zakhala zikulalikira kwanthaŵi yaitali kuti nkhondo zosakaza za m’zaka za zana lino, limodzi ndi zivomezi zambiri, miliri, njala, ndi zochitika zina, zonse pamodzi zimapereka umboni wakuti tili mu “masiku otsiriza”—nthaŵi yotsatira kuikidwa kwa Kristu monga Mfumu kumwamba m’chaka cha 1914.—Luka 21:10, 11; 2 Timoteo 3:1.
Mwa kugwiritsira ntchito Baibulo monga umboni wake, Nsanja ya Olonda imalengeza uthenga wabwino wakuti Ufumu wa Mulungu posachedwapa udzawononga otsendereza ndi kusandutsa dziko lapansi paradaiso. Ndipo bwanji ponena za nkhondo? Baibulo limati: “Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa padziko lapansi. Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta [a nkhondo] ndi moto.”—Salmo 46:8, 9.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Koloko: Mwa Chilolezo cha Imperial War Museum