Chitonthozo Mkati mwa Zaka Zinayi za Nkhondo
ANTHU ambiri anakumana ndi mavuto ndi njala yaikulu mkati mwa zaka zinayi za nkhondo kudera limene kale linali Yugoslavia. Ophatikizidwa pakati pawo anali Mboni za Yehova mazana ambiri, zimene zinapitiriza mokhulupirika kulambira “Mulungu wa chitonthozo chonse.”—2 Akorinto 1:3.
Ku Sarajevo, anthu anavutika ndi mavuto ena owonjezereka a kukhala ndi moyo mumzinda wina waukulu umene unali utazingidwa mkati mwa nkhondo yonseyo. Munalibe magetsi okwanira, madzi, nkhuni, ndi chakudya. Kodi mpingo wa Mboni za Yehova wa ku Sarajevo unali kuyenda motani m’mikhalidwe yovuta kwambiri imeneyi? Akristu a m’maiko oyandikana nawo anaika moyo wawo pangozi kuti apereke katundu wambiri wachithandizo. (Onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 1994, masamba 23-7.) Ndiponso, abalewo ku Sarajevo anali kugaŵana zimene anali nazo, akumaika mtima pa kugaŵana zinthu zauzimu. Mkati mwa kuzingidwako woyang’anira wina wachikristu wa ku mzinda umenewo anapereka lipoti lotsatirali:
“Timaŵerengera kwambiri misonkhano yathu. Ineyo ndi mkazi wanga, limodzi ndi anthu ena 30, timayenda mtunda wa makilomita 15 ulendo umodzi kumka kumisonkhano. Nthaŵi zina amalengeza kuti adzapereka madzi panthaŵi imene timachita misonkhano. Kodi abalewo amachitanji? Kodi amakhala panyumba kapena kupita ku misonkhano? Abale athu amasankha kupita ku misonkhano. Nthaŵi zonse abalewo amathandizana; amagaŵana chilichonse chimene ali nacho. Mlongo wina mumpingo wathu amakhala kunja kwa mzinda, kufupi ndi nkhalango; chotero nkosavuta kwambiri kupeza nkhuni. Amagwiranso ntchito m’bekale, ndipo malipiro ake amakhala a ufa wa tirigu. Pamene kuli kotheka kwa iye, amaphika mtanda waukulu wa buledi ndi kuubweretsa kumsonkhano. Msonkhano utatha, potuluka, amanyemera munthu aliyense.
“Chinthu chofunika nchakuti palibe aliyense wa abale kapena alongo amene amamva konse kukhala wosiyidwa. Palibe amene akudziŵa za aliyense wa ife amene adzatsatira kufuna thandizo mumkhalidwe wosavuta. Pamene kunali chipale m’misewu ndipo mlongo wina anali kudwala, abale achichepere ndi amphamvu anamkoka pa sleigh kumka naye kumisonkhano.
“Tonsefe timakhala ndi phande mu ntchito yolalikira, ndipo Yehova wadalitsa zoyesayesa zathu. Waona mkhalidwe wathu wa nsautso mu Bosnia, koma watidalitsa ndi chiwonjezeko—chiwonjezeko chimene sitinaonepo nkhondo isanayambe.”
Mofananamo, m’mbali zina zosakazidwa ndi nkhondo za amene kale anali Yugoslavia, Mboni za Yehova zapeza chiwonjezeko ngakhale kuti panali mavuto ochuluka. Ku ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Croatia kukuchokera lipoti ili lonena za kagulu kena ka Mboni: “Abale amene akukhala ku Velika Kladuša anakumana ndi nthaŵi za mavuto owopsa kuchita nawo. Tauniyo inaukiridwa nthaŵi zingapo. Abalewo anafunikira kufotokoza za uchete wawo ku magulu ankhondo achikrowesha, achisebiya, ndi magulu ankhondo osiyanasiyana achisilamu. Ndithudi, anafunikira kupirira zambiri—kuikidwa m’ndende, kumenyedwa, njala, ngozi ya imfa. Chikhalirechobe, onsewo anakhalabe okhulupirika ndipo ali ndi mwaŵi wapadera wa kuona dalitso la Yehova pa ntchito zawo.”
Ngakhale kuti panali mavuto ameneŵa, Mboni za Yehova ku Velika Kladuša ndi Bihać woyandikana naye zikupitiriza kupeza chiwonjezeko pamene mwachangu zikuuza anansi awo uthenga wotonthoza wa Mulungu. Ofalitsa Ufumu okwanira 26 a m’malo aŵiriwa akuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba 39!