Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 11/1 tsamba 32
  • “Tonsefe Tili a Banja Limodzi”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Tonsefe Tili a Banja Limodzi”
  • Nsanja ya Olonda—1996
Nsanja ya Olonda—1996
w96 11/1 tsamba 32

“Tonsefe Tili a Banja Limodzi”

M’ZAKA zaposachedwapa tsankhu la chipembedzo ndi utundu zafalikira padziko lonse. Kusiyana kwa mafuko kwabutsa kuphana, chizunzo, ndi nkhanza zina zonyazitsa. Malinga ndi lipoti la Amnesty International, mtopola pa zoyenera za munthu waumiriza anthu oposa mamiliyoni 23 padziko lonse kuthaŵa kwawo mu 1994.

M’Rwanda mokha, anthu 500,000 anaphedwa ndipo ena oposa 2,000,000 anakhala othaŵa kwawo pambuyo pa kuulika kwa chiwawa pakati pa Atutsi ndi Ahutu. “Makamaka Mboni za Yehova zinazunzidwa kwambiri,” inatero nyuzipepala ya ku Belgium Le Soir, “kaamba ka kukana kwawo kunyamula zida zankhondo.” Mboni za Yehova sizimaloŵerera m’nkhondo za zida. Komabe, mazana a iwo anaphedwa m’chiwawacho. Ichi chikutikumbutsa mawu a Yesu kwa ophunzira ake kuti: “Popeza simuli a dziko lapansi . . . chifukwa cha ichi likudani inu.”​—Yohane 15:19.

Banja lina la Mboni​—Eugène Ntabana, mkazi wake, ndi ana aŵiri​—linkakhala mumzinda waukulu, Kigali. Pofotokoza uchete wachikristu kwa anansi ake, Eugène kaŵirikaŵiri ankalankhula za bougainvillea, mphesa wotamba umene umakondwa m’madera ofunda.​—Mateyu 22:21.

“Muno mu Kigali,” Eugène ankafotokoza, “bougainvillea imatulutsa maluŵa ofiira, aupofu [pink] ndipo nthaŵi zina oyera. Komabe, onsewo ali a gulu limodzi. Zili chimodzimodzi ndi anthu. Ngakhale kuti tingakhale a mitundu yosiyana, maonekedwe a khungu, kapena mafuko, tonsefe tili a banja limodzi, banja la mtundu wa anthu.”

Mwatsoka, mosasamala kanthu za mkhalidwe wawo wamtendere ndi kaimidwe kauchete, banja la Antabana linaphedwa mwambanda ndi gulu losusukira kukhetsa mwazi. Komabe, iwo anafa ali okhulupirika. Tili otsimikizira kuti Yehova Mulungu adzakwaniritsa lonjezo lake kwa oterowo, ndipo iwo adzaukitsidwa kuti alandire dziko mmene tsankhu silidzakhalakonso. (Machitidwe 24:15) Pamenepo, banja la Antabana, limodzi ndi ena, “adzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—Salmo 37:11.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena