Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 11/15 tsamba 32
  • ‘Iwo Amakonda Kuthandiza Ena’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Iwo Amakonda Kuthandiza Ena’
  • Nsanja ya Olonda—1996
Nsanja ya Olonda—1996
w96 11/15 tsamba 32

‘Iwo Amakonda Kuthandiza Ena’

ZIMENEZO nzimene wapolisi wina mu mzinda wa New York ananena ponena za Mboni za Yehova. Anali kulankhula ndi Kathleen, mmodzi wa antchito odzifunira a nthaŵi zonse wotumikira pa malikulu a dziko lonse a Mboni za Yehova m’Brooklyn, New York.

Popuma masana, pa tsiku lofunda ndi la dzuŵa m’mphakasa, Kathleen anakhala pa benchi pa kapaki kapafupi. Anali kumvetsera kaseti pa wailesi yokhala ndi mahedifoni. Pa bwalo la mahelikopita patsidya la mtsinje wa East River, makonzedwe anali mkati oti papa anyamuke, yemwe anadzachezera mzindawo. Chitetezo chinali champhamvu paliponse, ndipo apolisi angapo anali kumalonda kapakiko. Mmodzi wa iwo anamfikira Kathleen ndi kumfunsa chimene iye anali kuchita. Kathleen anayankha kuti: “Ndikumvetsera tepi ya chinenero cha Chirasha. Mwaona nanga, ndine mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo ndikufuna kuphunzira Chirasha kotero kuti ndigaŵane uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi anthu olankhula Chirasha omwe abwera kudzakhala mu mzinda uno.”

Wapolisiyo anayankha kuti anadzafikira pakusirira Mboni za Yehova mkati mwa zaka 15 monga ofesala wachitetezo mu mzinda wa New York. Anatero kuti: “Ndimaona Mboni za Yehova monga chipembedzo cholinganizidwa chimene ziŵalo zake moona mtima zimakonda kuthandiza ena m’chitaganya.”

Mboni za Yehova nzodziŵika padziko lonse chifukwa cha ntchito yolalikira khomo ndi khomo imene zimachita. (Machitidwe 20:20) Pamene kuli kwakuti zimasonya ku Ufumu wa Mulungu monga njira yokha yothetsera mavuto amene akukantha mtundu wa anthu, izo zimathandizanso anthu kuwongolera khalidwe la moyo wawo mwa kuwalimbikitsa kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo m’moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, Mboni zimasonkhezera makolo kupangitsa nyumba zawo kukhala malo abwino ophunzirira. Zimalangiza anthu kukhala oona mtima ndi omvera malamulo, zikumawalimbikitsa kukulitsa maluso ndi mikhalidwe imene wolemba ntchito adzaona kukhala yamtengo wapatali.

Inde, Mboni za Yehova nzokondadi kuthandiza ena m’chitaganya kuti awongolere moyo wawo. Mukupemphedwa mwa chikondi kulandira mwaŵi woperekedwawu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena