Chilakiko Chinanso cha Mboni za Yehova ku Greece
PA October 6, 1995, mlandu wa atumiki aŵiri anthaŵi zonse a Mboni za Yehova unakambidwa ndi oweruza atatu m’khoti la mejasitiliti ku Athens. Mlanduwo unali wa kutembenuzira anthu ku chipembedzo china, ndipo yemwe anakasumayo anali wapolisi wina pambuyo pochezeredwa ndi Mboni kunyumba kwake.
Mafunso amene woweruza wotsogozayo anali kufunsa anasonyeza kuti anali wokondweretsedwa ndi ntchito ya Mboni za Yehova. Mwachitsanzo, anafunsa kuti: “Mwakhala mukuchita ntchito imeneyi kwa utali wotani? Kodi anthu anali kutani nanu m’zaka zonsezi? Kodi anthu anali kulabadira motani ntchito yanu? Kodi mumanenanji kwa anthu pamakomo awo?” Onse omwe anali m’khotimo anamvetsera ndi chidwi umboni wabwino umene unaperekedwa.
Chimene chinadabwitsa kwambiri Mbonizo chinali chakuti ngakhale loya wa boma analankhula mowayanja. “Mboni za Yehova zimaloledwa ndi lamulo osati chabe kukhulupirira Mulungu wawo ndi kumlambira iyayi,” anatero m’mawu ake otsiriza, “komanso kufalitsa chikhulupiriro chawo kukhomo ndi khomo, poyera, ndi m’misewu, ngakhale kugaŵira mabuku awo kwaulere ngati afuna kutero.” Loyayo anapereka zitsanzo zosiyanasiyana za kumasula mlandu zimene Bungwe la Boma ndi makhoti ananena. Ananenanso za mlandu wa Kokkinakis v. Greece, umene European Court of Human Rights (khoti la ku Ulaya la Zoyenera za Munthu) linagamula mokomera Mboni za Yehova.a “Chonde,” anachenjeza choncho loyayo, “zindikirani kuti Greece analipira faindi pamlandu umenewu. Chotero tiyenera kukhala osamala kwambiri tikapemphedwa kuweruza milandu yotereyi. Kapena ndingoti milandu yotereyi isamafike kukhoti kuno iyayi.”
Atatha kulankhula loya wa bomayo, panalibe zambiri zoti loya wa Mboni anenepo. Komabe, anangotenga mwaŵiwo ndi kugogomezera kuti lamulo la kuletsa kutembenuzira anthu kuchipembedzo china silinali loyenera ndipo likunyazitsa Greece pamaso pa maiko onse.
Woweruza wotsogozayo anangotembenukira kwa oweruza ena aŵiriwo, ndipo mbale ndi mlongoyo anamasulidwa nthaŵi imodzimodziyo. Kuzenga mlanduko, kumene kunatenga ola limodzi ndi mphindi khumi, kunali chilakiko cha dzina la Yehova ndi anthu ake omwe.
Kumeneku ndi kumasulidwa kwachinayi ponena za milandu ya kutembenuzira anthu kuchipembedzo china pambuyo pakukambidwa kwa mlandu wa a Kokkinakis m’European Court of Human Rights. Mboni za Yehova mu Greece nzosangalala chifukwa mavuto okhudza kulalikira kwawo tsopano atheratu ndi kuti nkotheka kupitiriza ntchitoyo popanda choletsa.
[Mawu a M’munsi]