Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 3/1 tsamba 32
  • Kodi Ndani Akuyendetsa Zinthu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Akuyendetsa Zinthu?
  • Nsanja ya Olonda—1997
Nsanja ya Olonda—1997
w97 3/1 tsamba 32

Kodi Ndani Akuyendetsa Zinthu?

“NDANI kodi akulamulira dziko?” Ngati wina anakufunsani funso limenelo, mukanamyankha bwanji? Anthu ambiri achipembedzo akanati “Mulungu” kapena “Yesu.” Nkhani ina ya m’nyuzipepala ya ku Bahamas, Freeport News, inapereka yankho limene ambiri sanaliyembekezere.

“Ndinapeza trakiti pansi pa chitseko changa,” wolemba nkhaniyo anayamba choncho. “Nthaŵi zonse sindimasamala timapepala toteroto, koma ulendo uno ndinasankha kukaŵerenga. Mutu wake unafunsa kuti, ‘Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko?’” Ataŵerenga trakiti lonena za Baibulo limeneli, mkazi ameneyu anadziŵa kuti wolamulira dzikoli si Mulungu kapena Yesu ayi koma Satana Mdyerekezi.​—Yohane 12:31; 14:30; 16:11; 1 Yohane 5:19.

“Talingalirani kupambanitsa m’kupha kwanjiru kokhetsa mwazi,” trakitilo linafotokoza choncho. “Anthu agwiritsira ntchito utsi wakupha, misasa yachibalo, malaŵi a moto oponyedwa, mabomba amoto, ndi njira zina zankhalwe kwadzaoneni kuzunza, ndi kuphana mwankhanza.  . . . Kodi ndi mphamvu ziti zimene zimasonkhezera anthu kuchita zinthu zonyansa zotero kapena kuwasonkhezera kuloŵa mumkhalidwe umene amakhala okakamizidwa kuchita nkhanza zotero? Kodi munayamba mwadabwa kuti kaya mphamvu ina yoipa, yosaoneka ikulamulira anthu kuchita zinthu zachiwawa zotero?” Kodi nzodabwitsa kuti Baibulo limamtcha Satana kuti “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano”?​—2 Akorinto 4:4.

Ndi bwino kuti nthaŵi yayandikira pamene Satana ndi ziŵanda zake sadzakhalakonso. “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.” (1 Yohane 2:17) Inde, Baibulo likulonjeza kuti amene amachita chifuniro cha Mulungu adzakhala ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo kosatha padziko lapansi lolungama. (Salmo 37:9-11; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4) Chisonkhezero choipa cha Satana ndi ziŵanda zake chitachotsedwa kudzakhala mpumulotu!

Atafotokoza mwachidule zamkati mwa trakiti laling’onolo, wolemba nkhani ya The Freeport News anamaliza mwa kunena kuti: “Ndasangalala zedi kuti ndinaliŵerenga trakiti limenelo . . . chifukwa inenso ndinali wodera nkhaŵa za mkhalidwe wa dzikoli, ndi yemwe akuyendetsa zinthu.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena