Olengeza Ufumu Akusimba
“Muŵalitse Inu Kuunika Kwanu Pamaso pa Anthu”
MU ULALIKI wake wa Paphiri, Yesu anati kwa ophunzira ake: “Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi.” Ndipo anawasonkhezeranso kuti: “Muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.”—Mateyu 5:14-16.
Ku Italy ntchito zabwino za Mboni za Yehova nzosabisika. Mwachitsanzo, khalidwe lawo labwino pamisonkhano yawo yachaka ndi chaka limatamanda Mulungu, monga mmene malipoti otsatiraŵa akusonyezera:
▪ Kwa zaka zambiri mkazi wina ku Terni, Italy, anali kuthandiza mwana wake wamkazi kuyendetsa kantini imene inali pafupi ndi bwalo la maseŵero mumzindawo. Akulongosola kuti: “Ndinaona kusiyana kwakukulu kwa aja amene anabwerera maseŵero ampira ndi nthumwi za pamsonkhano wa Mboni za Yehova kumeneko. Mbonizo zinavala molemekezeka kwambiri, ndipo zinali zoona mtima ndi zaulemu. Nthaŵi zonse ndimadabwa kuti kodi anthu osiyanasiyana mafuko ameneŵa amagwirizana bwanji chonchi.
“Tsiku lina Mboni ina inandiimika pamsewu nkundifunsa ngati ndinadziŵa dzina la Mulungu. Sindinalidziŵa, ndiye popeza kuti ndinadziŵa kuti Mboni za Yehova ndi anthu abwino, ndinalola kuti adzandichezere. Ndinali ndi mafunso onena za mkhalidwe wa akufa, ndipo anawayankha ndi Baibulo. Sindinazengereze iyayi, ndinavomereza kuphunzira Baibulo, ndipo milungu iŵiri pambuyo pake ndinayamba kupezeka pamisonkhano.
“Poyamba mwana wanga amanditsutsa, koma khalidwe langa ndi kutsimikiza kwanga kunasintha maganizo ake. Ndinayamba kuphunzira miyezi isanu ndi inayi yapitayo. Lero mwana wangayo ndi mwamuna wake amanena moyamikira Mboni zimene zimabwera kudzadya m’kantini yawo. Ponena za ine, ndinabatizidwa pamsonkhano wachigawo wina m’bwalo la maseŵero lomwelo.”
▪ Pambuyo pa msonkhano wachigawo mu Roseto degli Abruzzi, manijala wina wa kampu anati: “Ndaona kuti Mboni za Yehova nzoona mtima pazonse zimene zimachita. Mlungu wathawu, okwanira 40 anali ku kampu yanga ndipo sanavutitse iyayi. M’malo mwake, ndi okhawo amene amadzakuuza ngati pali munthu wina yemwe akugona m’ngolo yawo kapena hema wawo. Monga mmene ndikudziŵira, izo ndi makasitomala abwino kwambiri kukhala nawo.”
▪ Pambuyo pa msonkhano wachigawo umodzimodziwo, manijala wina wa hotela anati: “Mboni za Yehova zonse nzamtendere. Si zaphokoso, ndipo zimagona msanga. Ndi zaulemudi, zoona mtima, ndi zodzisunga bwino. Zikanakhala bwino ngati munthu aliyense akanakhala ngati izo. Ena amaba chilichonse—zoikamo maluŵa, mbale zaphulusa, ngakhale mapepala a m’chimbudzi ndi shuga! Inu simunachitepo zoterozo iyayi. Pamene ana anu atenga ice cream m’firiji madzulo, sindimadzivutitsa kuti ndikaone chimene atenga iyayi. Amaŵerengera okha mtengo ndipo amandilipira nthaŵi yomweyo. Ndimawadalira kwambiri. Zikanakhala bwino chotani nanga ngati ena akanakhala choncho! Ndingokhumba kuti alendo anga onse akanakhala Mboni za Yehova.”
Mboni za Yehova nzodziŵika bwino ku Italy, ngakhale m’mbali zina zadziko lapansi. ‘Mayendedwe awo mwa amitundu amakhala okoma’ chotero zimatamanda Mulungu woona, yemwe zimatchedwa ndi dzina lake.—1 Petro 2:12.