Kodi Zochitika Zonga Izi Zidzatichoka?
KULIKONSE kumene tingapite masiku ano, timaona udani, kulimbana, ndi nkhondo. Koma si cholinga cha magazini ino kuwonjezera uthenga woipa pa zimene mukudziŵa kale. M’malo mwake, kope lapadera limeneli lidzakudziŵitsani zoonadi ziŵiri zotonthoza. Choyamba, kuti maulosi akale omwe ali m’Baibulo ananeneratu zochuluka za uthenga woipa wokhumudwitsa m’nyengo yathu; chachiŵiri, kuti buku laulosi limodzimodzilo likuneneratu tsiku limene zochitika zonga chili pachithunzipa zidzakhala zakale. Sikudzakhalanso nkhondo. Sikudzakhalanso mabomba, kuomba mfuti, mabomba otchera pansi, kapena uchigaŵenga. Sikudzakhalanso ana amasiye ovutika kapena othaŵa kwawo opanda nyumba. Dziko la mtendere weniweni, wotonthoza mtima. Kodi mungakonde kuliona tsiku loterolo? Tikukulimbikitsani kupenda zimene Baibulo likunena. Mungapezemo chitonthozo chachikulu chimene simunayembekezepo.