Ndi Malonjezo Ayani Omwe Mungadalire?
MU 1893 gulu la anthu 74 oona za kakhalidwe ka anthu linasonkhana ku chionetsero cha Chicago World’s Fair kuti likambitsirane zamtsogolo (mbali yake ikusonyezedwa pamwambapa). Poyang’ana kutsogolo zaka 100 kufika mu 1993, analonjeza zotsatirazi: “Anthu ambiri azidzakhala kufika zaka 150.” “Ndende zidzachepa ndipo zisudzulo zidzaonedwa monga zosayenera.” “Boma lidzakhala losavutirapo kulamulira, popeza kupita patsogolo kumapangitsa zinthu kukhala zosavuta.”
Mofananamo, mu 1967 buku lotchedwa kuti The Year 2000 linalonjeza kuti: “Podzafika chaka cha 2000, mwachionekere makompyuta adzalingana ndi munthu, kumtsanzira kapenanso kumpambana pa nzeru zina ‘zaumunthu,’ mwina kuphatikizapo ngakhale pa luso la kulinganiza ndi kukonza zinthu.” “Ganizo lakuti maloboti otsikirapo mtengo azidzachita ntchito zambiri za pakhomo . . . lioneka kuti lidzatheka m’chaka cha 2000.”
Kusakhoza kwa mtundu wa anthu kudziŵiratu zodzachitika kutsogolo kumasiyana kwambiri ndi luso la kuzindikira la Mulungu. Mwachitsanzo, yerekezerani malonjezo otchulidwa pamwambapa ndi zimene Baibulo linaneneratu pafupifupi zaka mazana makumi aŵiri zapitazo ponena za m’tsiku lathu: “Anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.”—2 Timoteo 3:1-5.
Ulosi wa m’Baibulo wa “masiku otsiriza” umenewu ndi umodzi wa ambiri amene akwaniritsidwa m’tsiku lathu. Mawu a Mulungu ananeneratu kuti “chizindikiro” cha kukhalapo kwa Yesu chidzaphatikizapo nkhondo yadziko lonse, njala, miliri, zivomezi, ndiponso kulalikidwa kwa padziko lonse kwa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 24:3-14; Luka 21:11.
Malonjezo osalephereka a Mulungu anapangitsa mlembi wina wa Baibulo kalekale kunena kuti: “Pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasoŵapo mawu amodzi.”—Yoswa 23:14.
Ndithudi, tikhoza kutsimikizira kuti malonjezo onse a Mulungu posachedwa adzachitika. Ufumu wa Mulungu udzathetsa matenda, upandu, kumwerekera ndi mankhwala osokoneza bongo, njala, ndi nkhondo—dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. (Salmo 37:10, 11, 29; Chivumbulutso 21:3, 4) Mutha kukhala ndi chidaliro chakuti ulosiwu udzakwaniritsidwadi! Umachokera kwa Mlengi wathu, yemwe “sakhoza kunama.”—Tito 1:2; yerekezerani ndi Ahebri 6:13-19.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Cleveland State University Archive