Kukhalabe Namwali Muukwati?
POYESA kuchirikiza zonena zakuti Mariya anapitirizabe kukhala namwali muukwati wake ndi Yosefe, ambiri ojambula zithunzithunzi zapamanja ndi osemasema asonyeza Yosefe monga munthu wokalamba. Iwo analingalira kuti Yosefe kwenikweni anali ngati kholo kwa Mariya osati ngati mwamuna wake. Koma Papa John Paul II posachedwapa anapereka lingaliro losiyana ponena za nkhaniyo. Iye akuti Yosefe “sanali wokalamba panthaŵiyo.” M’malo mwake, “ungwiro wake wamkati, chipatso cha chisomo cha Mulungu, unamchititsa kukhala muukwati wake ndi Mariya mwachikondi chosaloŵetsapo kugonana.”
Ngati Mariya anafuna kukhalabe namwali kosatha, kodi nchifukwa ninji anatomeredwa? “Tinganene kuti,” papa akuyankha, “panthaŵi ya kutomerana kwawo, Yosefe ndi Mariya anamvana zoti akakhalebe namwali.”
Komabe, Baibulo likufotokoza nkhaniyi mosiyana. Nkhani ya Mateyu ikusonyeza kuti Yosefe ‘sanagone naye kufikira atabala mwana wamwamuna.’ (Mateyu 1:25, New American Bible ya Katolika) Yesu atabadwa, Mariya sanakhalebe namwali muukwati wake ndi Yosefe. Umboni wina wa zimenezi ndiwo wakuti pambuyo pake nkhaniyo ya Uthenga Wabwino ikusonyeza kuti Yesu anali ndi abale ndi alongo ake.—Mateyu 13:55, 56.
Chotero, pamene kuli kwakuti Baibulo limanena kuti Mariya anali namwali pamene anabala Yesu, palibe maziko onenera kuti anakhalabe namwali kwa moyo wake wonse ndi Yosefe.