Krisimasi Holide Yadziko Kapena Tsiku Lopatulika Lachipembedzo?
KU China amatchedwa Mwamuna Wokalamba wa Krisimasi. Ku United Kingdom, amatchedwa Tate wa Krisimasi. Anthu a ku Russia amagwiritsira ntchito dzina lakuti Agogo Aamuna a Chipale, ndipo ku United States, amatchedwa Santa Claus.
Ambiri amaona mwamuna wokalamba wachimwemwe ameneyu wokhala ndi mimba yaikulu ndi ndevu zoyera mbuu ngati chipale, monga Krisimasi yeniyeniyo. Komatu nzodziŵikanso bwino lomwe kuti Santa Claus ndi nthano yozikidwa pa miyambo ya bishopu wa ku Mura wa m’zaka za zana lachinayi (m’dziko limene tsopano likutchedwa Turkey).
Miyambo kaŵirikaŵiri yasonkhezera kwambiri zochitika za pachikondwerero, ndipo chikondwerero cha Krisimasi chimakhudzidwanso. Nthano ya Santa ndi imodzi mwa nthano zambirimbiri zonena za holide yotchuka. Pamene kuli kwakuti anthu ena amanena kuti miyambo ya pa Krisimasi imagwirizana ndi zochitika zolembedwa m’Baibulo, kunena zoona, yambiri mwa miyambo imeneyi inachokera kuchikunja.
Chitsanzo china ndi mtengo wa Krisimasi. Buku lotchedwa The New Encyclopædia Britannica likuti: “Kulambira mtengo, kofala pakati pa Azungu achikunja, kunapitirizabe ngakhale pamene iwo analoŵa Chikristu m’miyambo ya ku Scandinavia ya kukongoletsa nyumba ndi nkhokwe mwakugwiritsira ntchito mitengo imene simagwetsa masamba pokondwerera Chaka Chatsopano ncholinga chopitikitsa mdyerekezi ndi miyambo ya kuika mtengo wokhalamo mbalame panyengo ya Krisimasi.”
Kupanga nkhata za mtengo wa holly kapena mitengo ina imene simagwetsa masamba ndi mwambo winanso wochitika panyengo ya Krisimasi. Mwambo umenewu unazikidwanso kwambiri pa kulambira kwachikunja. Aroma akale anali kugwiritsira ntchito nthambi za mtengo wa holly pokongoletsa akachisi panyengo ya Saturnalia, phwando la masiku asanu ndi aŵiri lochitira Saturn, mulungu wa malimidwe, lochitika pakati penipeni pa nyengo yachisanu. Phwando limeneli lachikunja linatchukanso kwambiri chifukwa chakuti anthu anali kuchita phokoso ndi zonyansa mosadziletsa.
Mwambo wa pa Krisimasi wa kupsompsona kunsi kwa mphukira ya mtengo wa mistletoe (wosonyezedwa pano) kwa ena kungaoneke ngati njira yosonyezera chikondi, koma ndi mwambo umene unali kuchitika m’Nyengo Zapakati. A Druid a m’Britain wakale anali kukhulupirira kuti mtengo wa mistletoe unali ndi mphamvu yamatsenga; choncho, anali kuugwiritsira ntchito pofuna kudzitetezera ku ziŵanda, ntchiso, ndi zinthu zina zamatsenga. M’kupita kwa nthaŵi, anayamba kukhulupirira kuti ngati upsompsona kunsi kwa mtengo wa mistletoe ungapeze mwaŵi wa kukwatira. Mwambo umenewu ukuchitikabe mpaka lero pakati pa anthu ena m’nyengo ya Krisimasi.
Iyi ndi ina mwa miyambo yambirimbiri ya pa Krisimasi yamakono imene yasonkhezeredwa kapena kutengedwa ku ziphunzitso zachikunja. Komabe, mwina mungafune kudziŵa mmene zimenezi zinayambira. Kodi holide imene amati imalemekeza kubadwa kwa Kristu inagwirizana bwanji ndi miyambo yosakhala yachikristu? Chofunika kwambiri ndicho kudziŵa kuti kodi Mulungu amaiona motani nkhani imeneyi?
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Tsamba 3: Santa Claus: Thomas Nast/Dover Publications, Inc., 1978; mistletoe patsamba 3 pamodzi ndi chithunzi cha patsamba 4: Discovering Christmas Customs and Folklore lolembedwa ndi Margaret Baker, lofalitsidwa ndi Shire Publications, 1994