Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 5/1 tsamba 32
  • Bwanji Osadzakhala Nawo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bwanji Osadzakhala Nawo?
  • Nsanja ya Olonda—1998
Nsanja ya Olonda—1998
w98 5/1 tsamba 32

Bwanji Osadzakhala Nawo?

NDJAUKUA ULIMBA ali ndi zaka 73 zakubadwa, ndipo chaka chatha anayenda ulendo wa makilomita pafupifupi 450. Iye anayenda pansi mtunda wonsewo, ndipo anatha masiku 16 akuyenda.

Mwamuna wachikulire ameneyu anayenda ulendo wautali umenewu pofuna kuti akapezeke pa umodzi mwa misonkhano yachigawo yachaka ndi chaka ya Mboni za Yehova. Msonkhanowo utatha, atasangalala kwambiri ndiponso atalimbikitsidwa mwauzimu, iye anayendanso pansi kubwerera kunyumba​—masiku enanso 16. Kodi kuvutikirapo konseko kunalidi kofunikira? Inde, kunali kofunikiradi! Ndjaukua Ulimba wakhala akuyenda ulendo umenewu chaka ndi chaka kwa zaka zingapo.

Mwamuna ameneyu wa mu Afirika anali mmodzi mwa anthu oposa 15 miliyoni ochokera m’maiko oposa 230 amene anakapezeka pamisonkhano yachigawo ya Mboni za Yehova chaka chatha. Komabe, ambiri sanayende masiku ambiri kuti akafike pamalo a msonkhano wachigawo. Ambiri anayenda pamagalimoto, pamabasi, pasitima, kapena pandege. Kodi munali mmodzi wa iwo?

Mu 1998, misonkhano yachigawo idzachitikanso kuzungulira dziko lonse, makamaka m’chilimwe. Ngati akhala ndi thanzi labwino, Ndjaukua Ulimba mwina adzayendanso ulendo wautali wofananawo pofuna kuti akapezekepo. Iye ndi anthu ena mamiliyoni ambiri adzamvetsera programu yothandiza, yolimbitsa chikhulupiriro, ndiponso yotsitsimula mtima. Kwa onse amene adzapezekapo, msonkhano wachigawowo udzakhala chinthu chosaiŵalika m’chakachi. Tili okondwa kukupemphani kuti inunso mudzapezekepo. A Mboni za Yehova a kwanuko adzakhala osangalala kukuuzani za malo a msonkhano wachigawo wapafupi ndi kwanuko.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena