Makhalidwe Abwino Adzetsa Chitamando
NYUZIPEPALA ya ku Italy yotchedwa La Gazzetta del Mezzogiorno inayamikira Mboni za Yehova chifukwa chofalitsa nkhani yakuti “Matera—City of Unique Cave Dwellings.” (Matera—Mzinda wa Mapanga Okhalamo Ochititsa Chidwi) Nkhani imeneyi inatuluka m’magazini ya Galamukani! yachingelezi ya July 8, 1997, imene inafalitsidwa m’zinenero zambiri. Pakali pano, magazini ya Galamukani! ikutembenuzidwa m’zinenero 81 ndipo makope oposa 19 miliyoni amafalitsidwa padziko lonse. Nyuzipepalayo inanena kuti magazini ya Galamukani! inapambana m’chilimwe “pankhani yolengeza za mzindawu [wa Matera] ncholinga cha kupititsa patsogolo mbiri yake ndi luso lake lazopangapanga.”
Nyuzipepalayo inayamikira Mboni mogwirizana ndi Msonkhano Wachigawo wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu” umene unachitikira ku Matera mu 1997. Nkhaniyo inanena kuti Mboni “zinasonkhanitsa anthu 4,000 m’Bwalo la Maseŵero la XXI Settembre [mumzindamo] pakati penipeni pa nyengo yachilimwe ndiponso pamene kunali dzuŵa lotentha kwambiri; iwo anagwira ntchito yonse yoyeretsa, kupakanso utoto, ndi kukonzanso zinthu zina zofunika pabwalo limeneli lamaseŵero (makamaka zimbudzi zake) ndipo sanafune malipiro alionse, ndiponso anadzigulira zipangizo zonse zofunika.”
Mboni za Yehova zimayesetsa kukhala anansi abwino. (Mateyu 22:37-39) Iwo amatsatiranso uphungu wa m’Malemba wakuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti . . . akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.”—1 Petro 2:12.