Kodi Mungasiyanitse Chabwino ndi Choipa?
“Ineyo ndinapha nawo anthu 25. . . . Ndimalota za chochitikacho usiku uliwonse ndipo tsiku lililonse ndimaona masomphenya ake. Ndimangolota maloto oipa okhaokha. . . . Ndikapita kwinakwake ndimaona nkhope ya munthu wina imene imandikumbutsa anthu amene ndinapha. Zimangooneka ngati zenizeni, kungokhala ngati zangochitika kumene. . . . Ndimalephera kudzikhululukira pazimene ndinachita.”—V.S.
“Anachita kundiuza kuti ndikawononge adaniwo. . . . Sindinaganizepo za amuna, akazi ndi ana. . . . Panthaŵiyo ndinalingalira kuti ndinangochita zimene anandiuza ndipo ndikulingalirabe motero, ndiponso ndinatsatira zimene anandilamula. Choncho, ndikuona kuti sindinalakwe pochita zimenezo.”—W.C.
PA March 16, 1968, amuna aŵiri amene agwidwa mawu pamwambawo anachita nawo zinthu zimene pambuyo pake zinadzatchedwa upandu wankhondo woipitsitsa. Iwo pamodzi ndi asilikali ena, analoŵa m’mudzi wina waung’ono wa ku Vietnam ndipo anapha anthu wamba mazana ambiri—kuphatikizapo akazi, ana, ndiponso amuna okalamba. Koma taonani kuti asilikali aŵiriwo anakhudzidwa mosiyana. Msilikali woyamba akumva chisoni kwambiri ndi zimene anachita. Wachiŵiriyo akuona kuti anachita zoyenera. Kodi nchiyani chomwe chinapangitsa kuti anthu aŵiriwa akhale ndi malingaliro osiyana pomwe anachita zinthu zofanana?
Yankho lake nlokhudza chikumbumtima—mphamvu yomwe Mulungu anatipatsa kuti izitithandiza kupenda mosamalitsa posankha zochita ndi zolingalira zathu. Chikumbumtima ndicho chinthu chimene chimatithandiza kusiyanitsa chabwino ndi choipa.
Popanga zosankha, anthu ena amatsatira mawu akuti, “Chikumbumtima chanu chikutsogolereni.” Komabe, nzomvetsa chisoni kuti chikumbumtima sichikhala chodalirika nthaŵi zonse. Ndithudi, anthu ambiri alekerera ngakhale kuchita zinthu zoipa kwambiri, koma chikumbumtima chawo sichinawavutitse nkomwe. (Yohane 16:2; Machitidwe 8:1) Mngelezi wolemba mabuku Samuel Butler anati chikumbumtima “chimasiya kulankhula kwa anthu amene safuna kuchimvera.”
Kodi chikumbumtima chanu mungachikhulupirire? Yankho lake limadalira kwambiri mmene chikumbumtimacho munachiphunzitsira, monga momwe nkhani yotsatira idzafotokozera.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Malo a nkhondo pamwamba: U.S. Signal Corps photo