Chenjerani ndi Chisimoni!
SIMONI wa ku Samariya anali wolemekezeka kwambiri m’dera la kwawo. Anakhalako m’zaka za zana loyamba C.E., ndipo anthu anadabwa kwambiri ndi matsenga akewo. Kunena za iye iwo amati: “Uyu ndiye mphamvu ya Mulungu, yonenedwa Yaikulu.”—Machitidwe 8:9-11.
Komabe Simoni atakhala Mkristu wobatizidwa, anazindikira mphamvu yaikulu kwambiri yoposa imene anali nayo kale. Inali mphamvu imene inapatsidwa kwa atumwi a Yesu, kuti nawo athe kupatsa ena mphatso zozizwitsa za mzimu woyera. Simoni anachita chidwi kwambiri motero kuti anapereka ndalama kwa atumwi ndi kuwapempha kuti: “Ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti amene aliyense ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera.”—Machitidwe 8:13-19.
Mtumwi Petro anadzudzula Simoni, nanena: “Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama. Ulibe gawo kapena cholandira ndi mawu awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu.”—Machitidwe 8:20, 21.
Pankhani ya Baibulo imeneyi ndi pamene pakuchokera liwu loti “chisimoni,” limene likutanthauza “tchimo la kugula kapena kugulitsa malo ngakhalenso kukwezedwa m’tchalitchi.” The New Catholic Encyclopedia ikuvomereza kuti makamaka kuyambira m’zaka za zana la 9 mpaka la 11 “chisimoni chinali chofala pakati pa amonke, atsogoleri achipembedzo amaudindo aang’ono, mabishopu, ngakhalenso apapa.” The Encyclopædia Britannica yachisanu ndi chinayi (1878) ikuti: “Kuphunzira mbiri ya zisankho zosankha Papa kumatsimikizira wophunzira kuti palibe chisankho chimene chinachitikapo popanda kuloŵetsamo chisimoni, pamene kuli kwakuti nthaŵi zambiri chisimoni chochitidwa m’zisankhozo chakhala choipitsitsa, chosachititsa manyazi, ndiponso chosabisa.”
Akristu oona lerolino ayenera kuchenjera ndi chisimoni. Mwachitsanzo, ena angamapereke thamo mopambanitsa kapena mphatso zochuluka kwa amene angawapatse maudindo owonjezereka. Kapenanso, amene angapereke maudindo amenewa angakondere awo amene angakhoze—komanso ofunitsitsa—kuwapatsa mphatso. Mbali zonsezi ndi chisimoni, ndipo Malemba momveka bwino amaletsa machitidwe oterewa. “Chifukwa chake lapa choipa chako ichi,” Petro analimbikitsa motero Simoni, “pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe cholingirira cha mtima wako. Pakuti ndiona kuti wagwidwa ndi ndulu yoŵaŵa ndi nsinga ya chosalungama.”—Machitidwe 8:22, 23.
Ubwino wake Simoni anazindikira kuopsa kwa chikhumbo chake cholakwikacho. Anapempha atumwiwo kuti: “Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.” (Machitidwe 8:24) Mwakutengapo phunziro lofunika pankhaniyi, Akristu oona amayesetsa kupewa kuipitsidwa kulikonse ndi chisimoni.