Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 12/1 tsamba 32
  • Chikondi Cholimba Kuposa cha Mayi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikondi Cholimba Kuposa cha Mayi
  • Nsanja ya Olonda—1998
Nsanja ya Olonda—1998
w98 12/1 tsamba 32

Chikondi Cholimba Kuposa cha Mayi

AMAYI akutaya ana awo obadwa kumene pa masiteshoni a sitima zoyenda pansi pa nthaka, m’zimbudzi za onse, ngakhalenso m’misewu ya anthu ambiri. Nthaŵi zina, otenga zinyalala apeza timakanda ngakhale m’mabini titatopa kulirira amayi awo. Malinga ndi O Estado de S. Paulo, “nkhani zotaya ana m’makwalala zikuwonjezeka.” Ndithudi, mayi wachitsikana angamve chisoni pambuyo pake ndi zimene anachita. Koma akutayabe khanda lakelo, ngakhale kuti zingatayitse moyo wa mwanayo.

Mungadzifunse kuti, ‘Kodi zitheka bwanji kuti mayi nkuganiza zotaya mwana pamalo amene sadziŵa chimene chidzamchitikira?’ Baibulo limagwiritsa ntchito mkhalidwe womvetsa chisoni umenewu monga fanizo posonyeza kusiyana kwakukulu ndi mmene Mlengi wathu amamvera kulinga kwa anthu ake: “Kodi mkazi angaiŵale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde awa angaiŵale, koma Ine sindingaiŵale iwe.”​—Yesaya 49:15.

Ndithudi, koposa mayi aliyense waumunthu, Mulungu ali ndi chikondi chenicheni kwa ife ndiponso amazindikira zosoŵa zathu. Kaya ndinu wachinyamata kapena wachikulire, kaya muli ndi vuto lotani, simuli nokha. Mlengi wanu akufuna kukuthandizani ndipo amafuna kuti muzikhala bwino. Mawu a wamasalmo amati, “pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.”​—Salmo 27:10.

Padziko lonse, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amafalitsidwa kupereka chidziŵitso cha “Mulungu woona yekha,” Yehova, ndi Mwana wake, Yesu Kristu, chimene chingapatse moyo wosatha awo amene amachilandira mosangalala.​—Yohane 17:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena