‘Aatali Ngati Mkungudza wa ku Lebano’
M’mapiri okongola a ku Lebano muli mitengo yodziŵika kuti Arz Ar-rab, kutanthauza “Mikungudza ya Ambuye.” Mitengo yokongola yosayoyoka masamba imeneyi, imene kale inakuta mapiriwo, imatchulidwa nthaŵi ngati 70 m’Baibulo—kuposa mtengo wina uliwonse.
Pofotokoza mikungudza ikuluikulu ya ku Lebano, Malemba amagwiritsa ntchito mawu akuti “okometsetsa” ndi “wokoma.” (Nyimbo ya Solomo 5:15; Ezekieli 17:23) Kuyambira nthaŵi zakale, ukulu wa mkungudza ndi kulimba kwa matabwa ake zaupangitsa kukhala wokondeka pomanga nyumba ndi zombo ngakhalenso popanga mipando. Kununkhira kwake ndi kufiirira kwa matabwa ake n’kochititsa kaso, ndipo popeza kuti uli ndi mamina ambiri, mtengowo sufumbwa kapena kuwonongedwa ndi tizilombo. Mitengoyo imatalika ndi kukula kwadzaoneni, kufika pautali wamamita ngati 37 ndi kukula m’mimba mamita ngati 12, ndipo ili ndi mizu yakuya ndi yolimba. Ndiye chifukwa chake osamalira nkhalango ena amakono amati mitengoyo ndiyo “ulemerero wa zomera”!
Wolemba Baibulo Ezekieli anayerekezera Mesiya mwaulosi kukhala nsonga ya mkungudza, wodzalidwa ndi Mulungu iyemwini. (Ezekieli 17:22) Kwenikweni, liwu lachihebri lotanthauza “mkungudza” limachokera kutsinde lotanthauza “kulimba.” Lerolino, otsatira Mesiya, Yesu Kristu, nawonso amayenera ‘kuchirimika m’chikhulupiriro, . . . kulimba,’ monga mtengo wautali ndiponso wolimba wa mkungudza. (1 Akorinto 16:13) Kodi angathe motani kuchita zimenezi? Mwa kukana motsimikiza mtima zisonkhezero zosakhala zachikristu ndi kupirira molimbika posunga umphumphu ndi kudzipereka kwaumulungu. Awo amene amachita zimenezo amafotokozedwa m’Baibulo kukhala “olungama . . . [amene amatalika] ngati mkungudza wa ku Lebano.”—Salmo 92:12, The New English Bible.