Tsiku Loyenera Kulikumbukira
Madzulo a tsiku loti maŵa lake akafa, Yesu anapereka mkate wopanda chotupitsa ndi chikho cha vinyo kwa atumwi ake ndipo anawauza kuti adye ndi kumwa. Anawauzanso kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.”—Luka 22:19.
Chaka chino tsiku lokumbukira chochitika chimenechi ndi Lachinayi, April 1, dzuŵa litaloŵa. Mboni za Yehova padziko lonse lapansi zidzasonkhana usiku wapadera umenewu ndi kuchita Chikumbutso chimenechi m’njira imene Yesu analamula. Mukuitanidwa ndi mtima wonse kudzakhala nafe. Chonde funsani Mboni za Yehova kwanuko kuti zikuuzeni nthaŵi ndi malo a msonkhano wapadera umenewu.