Kodi Moyo M’maukonda?
“Ndiloleni ndione kuŵala.” Ameneŵa ndi mawu omwe wolemba ndakatulo wina wa ku Italy Giacomo Leopardi analankhula kwa omwe anali kum’dwazika atangotsala pang’ono kumwalira. Mawuŵa akusonyeza kuti munthu amakonda kukhalabe ndi moyo, womwe munthuyu anauyerekeza ndi kuŵala.
Kufunitsitsa kukhalabe ndi moyo n’chilakolako chachibadwa, ndiponso chamtengo wapatali zedi chomwe chimasonkhezera ambiri kupeŵa ngozi ndi kuchita zilizonse mmene angathere kuti apitirizebe kukhala ndi moyo. Mwa ichi, munthu sakusiyana kwenikweni ndi nyama, zomwenso mwachibadwa zimafunitsitsa zitakhala ndi moyo.
Koma kodi ndi moyo wamtundu wanji umene ungafunikiredi kukhala wosangalatsa ndi wokondeka? Sikukhalako chabe kwa thupi—kapena kupuma ndi kumayenda basi. Ngakhalenso lingaliro lofuna kupeza zochuluka mmene munthu angathere m’moyo, silimakhutiritsa anthu. Nthaŵi zonse, maganizo a Aepikureya akuti, “tidye timwe pakuti mawa timwalira,” sanakhutiritse anthu. (1 Akorinto 15:32) Ngakhale kuti munthu mwachionekere wapeza zofunika zina zazikulu zakuthupi, amafunikirabe zinthu zokhudza chikhalidwe chabwino ndi zosangalatsa. Kuwonjezera pazimenezo, amafunikiranso zinthu zauzimu, zokhudzana ndi chikhulupiriro mwa Wam’mwambamwamba. N’zachisoni kuti anthu mamiliyoni, kapenanso mabiliyoni, akusoŵa mtendere chifukwa cha kupsinjika ndi mavuto okhudza chikhalidwe ndi malo m’madera ambiri padziko lapansi. Awo amene amangofuna kuti akhutiritse zokhumba zawo m’zinthu zakuthupi—kudya, kumwa, kukhala ndi chuma chochuluka, ngakhalenso kukhutiritsa chilakolako chawo cha kugonana—amangokhala ndi moyo monga wa nyama, ndipo sumakhutiritsa kwenikweni. Kwenikweni, iwo samagwiritsa ntchito mwayi waukulu womwe moyo wapereka kuti akwaniritse luntha ndi malingaliro abwino aumunthu. Kuwonjeza pamenepo, aliyense amene amakhumba kukhutiritsa zilakolako zake modzikonda, samapeza chilichonse chabwino m’moyo, komanso amawononga chikhalidwe cha anthu amene akukhala nawo, ndipo samathandizanso anzawo pa zosoŵa zawo.
Poikira umboni pa zimenezi, woweruza milandu ya ana anati “mavuto a zachikhalidwe, kutchukitsa anthu a zitsanzo zoipa, ndi kupeza chuma m’njira zachidule zosayenera” n’zimene “zimalimbikitsa mzimu wopikisana mopitirira muyeso.” Zimenezi zimayambitsa mikhalidwe yowononga chikhalidwe komanso yovulaza achinyamata, makamaka pamene ayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.
Mukudziŵa kuti moyo uli ndi zosangalatsa zambiri—Kupita m’malo osangalatsa patchuthi, kuŵerenga kapena kupanga kafukufuku wosangalatsa, maubwenzi abwino, nyimbo zokoma. Ndiponso pali zochita zina zomwe zimakhutiritsa kwambiri kapena pang’ono. Amene ali ndi chikhulupiriro chozama mwa Mulungu, kwenikweni mwa Mulungu wa m’Baibulo, Yehova, ali ndi zifukwa zambiri zoukondera moyo. Chikhulupiriro chenicheni ndicho gwero la mphamvu ndi bata zomwe zingathandize anthu kuchita ndi nthaŵi zovuta. Okhulupirira Mulungu woona, mwachidaliro anganene kuti: “Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa.” (Ahebri 13:6) Anthu amene amadziŵa bwino za chikondi cha Mulungu, amadzimva kuti iye amaŵakonda. Amachitapo kanthu posonyeza kuyamikira chikondi chake, ndipo amasangalala nacho. (1 Yohane 4:7, 8, 16) Angakhale ndi moyo wokangalika ndi wosadzitukumula womwenso uli maziko a chikhutiro. Zili monga mmene Yesu Kristu ananenera kuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
N’zachisoni kuti palinso mbali ina m’moyo umene tikukhalawu. Pali mavuto ochuluka, chisalungamo, umphaŵi, matenda, ndi imfa—kungotchulapo zochepa zokha mwa zopweteka zambiri zomwe kaŵirikaŵiri zimapangitsa moyo kukhala wosautsa. Mfumu Solomo, ya mtundu wakale wa Israyeli, pokhala yachuma, yamphamvu ndi yanzeru, sinasoŵe kanthu kosangalatsa munthu. Koma, panali kanthu kena komwe kanam’vutitsa maganizo kwambiri—kuzindikira kuti pa imfa adzasiyira munthu wina ‘ntchito zake zonse anasauka nazo,’ zimene anazichita “mwanzeru ndi modziŵa nadzipinduliramo.”—Mlaliki 2:17-21.
Monga Solomo, ambiri amadziŵa kuti moyo n’ngwakanthaŵi ndipo umatha mofulumira. Malemba amati Mulungu ‘anaika zamuyaya m’mitima yathu.’ (Mlaliki 3:11) Lingaliro la umuyaya limeneli limasonkhezera anthu kusinkhasinkha chifukwa chake moyo n’ngwaufupi chomwechi. Pambuyo pake, wina polephera kupeza mayankho okhutiritsa ponena za cholinga cha moyo ndi imfa, angasautsike pokhala ndi maganizo akuti moyo ndi woipa ndiponso wopanda pake. Zimenezi zingapangitse moyo kukhala womvetsa chisoni.
Kodi pali mayankho ku mafunso osautsa anthu otero? Kodi mikhalidwe yopangitsa moyo kukhala wosangalatsa ndi wokhalitsa idzakhalakodi?