‘Ngati Mchere Usukuluka’
NKHONDO zamenyedwa chifukwa cha iwo. Wagwiritsidwa ntchito ngati chosinthanitsira zinthu. Kale ku China, mtengo wake unali wachiŵiri kwa golide. Inde, kuyambira kale, anthu akhala akuona mchere monga chinthu cha mtengo wapamwamba kwambiri. Mpaka lero, umadziŵidwa kuti umatha kuchiritsa matenda ena ndi kupha tizilombo toyambitsa mafinya, ndipo ukugwiritsidwa ntchito padziko lonse monga chokoleretsera zakudya ndiponso ngati choteteza zinthu kuti zisavunde.
Malinga ndi maubwino ambiri a mchere ndi ntchito zake, ndi posadabwitsa kuti umagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa m’Baibulo. Chilamulo cha Mose, mwachitsanzo, chimafuna kuti chilichonse choperekedwa pa guwa la nsembe kwa Yehova chithiridwe mchere. (Levitiko 2:13) Cholinga chake sichinali kuwonjezera kukoma kwa nsembe, koma makamaka chifukwa chakuti mchere unkaphiphiritsa chiyero kapena kusavunda kwa nsembeyo.
Mu Ulaliki wake wa pa Phiri wotchukawo, Yesu Kristu anauza otsatira ake kuti: “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi.” (Mateyu 5:13) Ndi mawu ameneŵa, Yesu anasonyeza kuti kulalikira kwawo ponena za Ufumu wa Mulungu kukakhala ndi mphamvu ya kuteteza, kapena kupulumutsa miyoyo, ya amene akawamvera. Inde, awo amene anatsatira mawu a Yesu anatetezeka ku kuvunda kwakhalidwe ndi kwauzimu kumalo komwe ankakhala ndi kutumikirako.—1 Petro 4:1-3.
Komabe, Yesu anapitiriza ndi kuchenjeza: “Koma mcherewo ngati ukasukuluka, . . . pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.” Pothirira ndemanga pa mawu ameneŵa, katswiri wamaphunziro a Baibulo Albert Barnes ananena kuti mchere womwe Yesu ndi ophunzira ake ankadziŵa “unali wophatikizika ndi zinthu zina, wosakanizananso ndi zitsotso za zomera zina ndi dothi.” Tsono mcherewo utasukuluka, “dothi lokhalokha” ndilo lingatsale. “Zimenezi,” Barnes anatero, “zinalibe ntchito kupatulapo . . . kuzimwaza m’timisewu, monga mmene timachitira ndi miyala.”
Mwakumvera chenjezo limeneli, Akristu afunikira kuonetsetsa kuti sakuleka kuchita umboni poyera kapena kuti sakubwerera ku mayendedwe osaopa Mulungu. Apo ayi, angasukuluke mwauzimu ndi kukhala opanda ntchito, monga ‘mchere umene wasukuluka.’